A A A A A


Sakani

MATEYU 4:16
Anthu akukhala mumdima Adaona kuwala kwakukuru, Ndi kwa iwo okhala m'malo mthunzi wa imfa, Kuwala kunaturukira iwo.


MATEYU 10:21
Ndipo mbale adzapereka mbale wace kuimfa, ndi atate mwana wace: ndipo ana adzatsutsa akuwabala, nadzawafetsa iwo.


MATEYU 16:28
Indetu ndinena kwa inu, kuti alipo ena a iwo aima pane sadzalawa ndithu imfa, kufikira adzaona Mwana wa munthu atadza mu ufumu wace.


MATEYU 20:18
Onani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kwa ansembe akuru ndi alembi, ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa,


MATEYU 26:38
Pamenepo ananena kwa iwo, Moyo wanga uti wozingidwa ndi cisoni ca kufika naco kuimfa; khalani pano mucezere pamodzi ndi Ine.


MARKO 9:1
Ndipo ananena nao, Ndithu ndinena ndi inu kuti, Alipo ena akuimirira pano, amene sadzalawa imfa konse, kufikira akaona Ufumu wa Mulungu utadza ndi mphamvu.


MARKO 10:33
nati, Taonani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kwa ansembe akuru ndi alembi; ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa, nadzampereka Iye kwa anthu a mitundu;


MARKO 14:34
Ndipo ananena nao, Moyo wanga uli wa cisoni cambiri, kufikira imfa. Bakhalani pano, nimudikire.


LUKA 1:79
22 Kuwalitsira iwo okhala mumdima ndi mthunzi wa imfa; Kulunjikitsa mapazi athu mu njira ya mtendere.


LUKA 2:26
Ndipo anamuululira Mzimu Woyera kuti sadzaona imfa, kufikira adzaona Kristu wace wa Ambuye.


LUKA 9:27
Koma Ine ndinena ndi inu zoonadi, Kuli ena a iwo akuimirira pano, amene sadzalawatu imfa, kufikira kuti adzaona Ufumu wa Mulungu.


LUKA 22:33
Ndipo anati kwa iye, Ambuye, ndiripo ndikapite ndi Inu kundende ndikuimfa.


LUKA 24:20
ndikuti ansembe akulu ndi akulu athu anampereka iye ku ciweruziro ca imfa, nampacika iye pamtanda.


YOHANE 4:47
Iyeyu, pamene anamva kuti Yesu wacokera ku Yudeya nafika ku Galileya, ananka kwa iye, nampempha kuti atsike kukaciritsa mwana wace; pakuti anali pafupi imfa.


YOHANE 5:24
Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira iye amene anandituma Ine, ali nao moyo wosatha, ndipo salowa m'kuweruza, koma wacokera kuimfa, nalowa m'moyo.


YOHANE 8:51
Indetu, indetu, ndinena ndi inu, 9 Munthu akasunga mau anga, sadzaona imfa nthawi yonse.


YOHANE 8:52
Ayuda anati kwa Iye, Tsopano tazindikira kuti muli ndi ciwanda. 10 Abrahamu anamwalira, ndi aneneri; ndipo Inu munena, Munthu akasunga mau anga, sadzalawa imfa ku nthawi yonse.


YOHANE 11:4
Koma Yesu pamene anamva, anati, Kudwala kumene sikuli kwa imfa, koma cifukwa ca ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe nako.


YOHANE 11:13
Koma Yesu adanena za imfa yace; koma iwowa anayesa kuti ananena za mpumulo wa tulo.


YOHANE 12:33
Koma ananena ici ndi kuzindikiritsa imfa yanji akuti adzafa nayo.


YOHANE 18:32
kuti mau a Yesu akwaniridwe, amene ananena akuzindikiritsa imfa imene, akuti adzafa nayo.


YOHANE 21:19
Koma ici ananena ndi kuzindikiritsa imfa imene adzalemekeza nayo Mulungu. Ndipo m'mene ananena ici, anati kwa iye, nditsate Ine,


MACHITIDWE A ATUMWI 2:24
yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti iye agwidwe nayo.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:1
Ndipo Saulo analikubvomerezana nao pa imfa yace. Ndipo tsikulo kunayamba kuzunza kwakukuru pa Mpingo unali m'Yerusalemu; ndipo anabalalitsidwa onse m'maiko a Yudeya ndi samariya, koma osati atumwi ai.


Skutky Apoštolské 22:4
ndipo ndinalondalonda Njira iyi kufikira imfa, ndi kumanga ndi kupereka kundende amuna ndi akazi.


Skutky Apoštolské 23:29
Ndipo ndinapeza kuti adamnenera za mafunso a cilamulo cao; koma analibe kumnenera kanthu kakuyenera imfa kapena nsinga.


Skutky Apoštolské 25:11
Pamenepo ngati ndiri wocita zoipa, ngati ndacita kanthu kakuyenera imfa, sindikana kufa; koma ngati zinthuzi awa andinenera nazo ziri zacabe, palibe mmodzi akhoza kundipereka kwa iwo. Nditurukira kwa Kaisara.


Skutky Apoštolské 25:25
Koma ndinapeza ine kuti sanacita kanthu, koyenera imfa iye; ndipo popeza, iye yekha anati akaturukire kwa Augusto, ndatsimikiza mtima kumtumizako.


Skutky Apoštolské 26:31
ndipo atapita padera analankhula wina ndi mnzace, nanena, Munthu uyu sanacita kanthu koyenera imfa, kapena nsinga.


1 AKORINTO 3:22
ngati Paulo, kapena Apolo, kapena Kefa, kapena dziko apansi, kapena moyo, kapena imfa, capena za makono ano, kapena drinkudza; zonse ndi zanu;


1 AKORINTO 11:26
Pakuti nthawi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera cikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza iye.


1 AKORINTO 15:21
Pakuti monga imfa inadza mwa munthu, kuuka kwa akufa kunadzanso mwa munthu.


1 AKORINTO 15:26
Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.


1 AKORINTO 15:53
Pakuti cobvunda ici ciyenera kubvala cisabvundi, ndi 19 caimfa ici kubvala cosafa.


1 AKORINTO 15:54
Ndipo pamene cobvunda ici cikadzabvala cisabvundi ndi caimfa ici cikadzabvala cosafa, pamenepo padzacitika mau olembedwa, 20 Imfayo yamezedwa m'cigonjetso.


1 AKORINTO 15:55
21 Imfawe, cigonjetso cako ciri kuti? Imfawe, mbola yako iri kuti?


1 AKORINTO 15:56
Koma mbola ya imfa ndiyo ucimo; koma 22 mphamvu ya ucimo ndiyo cilamulo:


2 AKORINTO 1:9
koma tokha tinakhala naco citsutso ca imfa mwa ife tokha, kuti tisalimbike pa ife tokha, koma pa Mulungu wakuukitsa akufa;


2 AKORINTO 1:10
amene anatilanditsa mu imfa yaikuru yotere, nadzalanditsa;


2 AKORINTO 2:15
Pakuti ife ndife pfungo labwino la Kristu, kwa Mulungu, mwa iwo akupulumutsidwa, ndi mwa iwo akuonongeka; kwa ena pfungo la imfa kuimfa;


2 AKORINTO 3:7
Komangati utumiki wa imfa wolembedwa ndi wolocedwa m'miyala, unakhala m'ulemerero, kotero kuti ana a Israyeli sanathe kuyang'anitsa pankhope yace ya Mose, cifukwa ca ulemerero wa nkhope yace, umene unalikucotsedwa:


2 AKORINTO 4:11
Pakuti ife amene tiri ndi moyo tiperekeka kuimfa nthawi zonse, cifukwa ca Yesu, kuti moyonso wa Yesu uoneke m'thupi lathu lakufa.


2 AKORINTO 4:12
Cotero imfa icita mwa ife, koma moyo mwa inu.


2 AKORINTO 5:4
Pakutinso ife okhala mu msasawu tibuula, pothodwa; si kunena kuti tifuna kubvulidwa, koma kubvekedwa, kuti caimfaco cimezedwe ndi moyo.


2 AKORINTO 7:10
Pakuti cisoni ca kwa Mulungu citembenuzira mtima kueipulumutso, cosamvetsanso cisoni; koma cisonicadziko lapansi cicita imfa.


2 AKORINTO 11:23
Kodi ali atumiki a Kristu? (ndilankhula monga moyaruka), makamaka ine; m'zibvutitso mocurukira, m'ndende mocurukira, m'mikwingwirima mosawerengeka, muimfa kawiri kawiri.


AFILIPI 1:20
monga mwa kulingiriritsa ndi ciyembekezo canga, kuti palibe cinthu cidzandicititsa manyazi, komatu mwa kulimbika mtima konse, monga nthawi yonse, tsopanonso Kristu adzakuzidwa m'thupi langa, kapena mwamoyo, kapena mwa imfa.


AFILIPI 2:8
ndipo popezedwa m'maonekedwe ngati munthu, anadzicepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.


AFILIPI 2:27
Pakutinso anadwaladi pafupi imfa; komatu Mulungu anamcitira cifundo; koma si iye yekha, komatu inenso, kuti ndisakhale naco cisoni cionjezere-onjezere.


AFILIPI 2:30
pakuti cifukwa lea nchito ya Kristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wace, kuti z akakwaniritse ciperewero ca utumiki wanu wa kwa ine.


AFILIPI 3:10
kuti ndimzindikire iye, ndi mphamvu ya kuuka kwace, ndi ciyanjano ca zowawa zace, pofanizidwa ndi imfa yace;


AKOLOSE 1:22
m'thupi lace mwa imfayo, kukaimika inu oyera, ndi opanda cirema ndi osatsutsika pamaso pace;


2 TIMOTEO 1:10
koma caonetsedwa tsopano m'maonekedwe a Mpulumutsi wathu Kristu Yesu, amenedi anatha imfa, naonetsera poyera moyo ndi cosabvunda mwa Uthenga Wabwino,


AHEBRI 2:9
Koma timpenya iye amene adamcepsa pang'ono ndi angelo, ndiye Yesu, cifukwa ca zowawa za imfa, wobvala korona wa ulemerero ndi ulemu, kuti ndi cisomo ca Mulungu alawe imfa m'malo mwa munthu ali yense.


AHEBRI 2:14
Popeza tsono ana ndiwo a mwazi ndi nyama, Iyenso momwemo adalawa nao makhalidwe omwewo kuti mwa imfa akamuononge iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye mdierekezi;


AHEBRI 2:15
nakamasule iwo onse amene, cifukwa ca kuopa imfa, m'moyo wao wonse adamangidwa ukapolo.


AHEBRI 5:7
Ameneyo, m'masiku a thupi lace anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukuru ndi misozi kwa iye amene anakhoza kumpulumutsa iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,


AHEBRI 7:23
Ndipo iwo ndiwo ambiri anakhala ansembe, popeza imfa idawaletsa asakhalebe;


AHEBRI 9:15
Ndipo mwa ici ali Nkhoswe ya cipangano catsopano, kotero kuti, popeza kudacitika imfa yakuombola zolakwa za pa cipangano coyamba, oitanidwawo akalandire lonjezano la zolowa zosatha.


AHEBRI 9:16
Pakuti pamene pali copangiratu pafunika pafike imfa ya wolemberayo.


AHEBRI 11:5
Ndi cikhulupiriro Enoke anatengedwa kuti angaone imfa; ndipo sanapezeka, popeza Mulungu adamtenga: pakuti asanamtenge, anacitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu;


YAKOBO 1:15
Pamenepo cilakolakoco citaima, cibala ucimo; ndipo ucimo, utakula msinkhu, ubala imfa.


YAKOBO 5:20
azindikire, kuti iyeamene abweza wocimwa ku njira yace yosocera adzapulumutsa munthu kwa imfa, ndipo adzabvundikira macimo aunyinji.


1 YOHANE 3:14
Ife tidziwa kuti tacokera kuturuka muimfa kulowa m'moyo, cifukwa tikondana ndi abale iye amene sakonda akhala muimfa.


1 YOHANE 5:16
Wina akaona mbale wace alikucimwa cimo losati la kuimfa, apemphere Mulungu, ndipo iye adzampatsira moyo wa iwo akucita macimo osati a kuimfa. Pali cimo la kuimfa: za ililo sindinena kuti mupemphere.


1 YOHANE 5:17
Cosalungama ciri conse ciri ucimo; ndipo pali cimo losati la kuimfa.


CHIVUMBULUTSO 1:18
ndi Wamoyoyo; ndipo 1 ndinali wakufa, ndipo taona, ndiri wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndiri nazo zofungulira za imfa ndi Hade.


Revelation 2:10
Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena ainu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala naco cisautso masiku khumi. Khala wokholupirfka kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.


Revelation 2:11
Iye wokhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo. Iye amene alakika sadzacitidwa coipa ndi imfa yaciwiri.


Revelation 2:23
Ndipo ndidzaononga ana ace ndi imfa; ndipo idzazindikira Mipingo yonse kuti 3 ine ndine iye amene ayesa imso ndi mitima; ndipo 4 ndidzaninkha kwa yense wa inu monga mwa nchito zanu.


Revelation 6:8
Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wotumbuluka; ndipo iye womkwera, dzina lace ndiye Imfa; ndipo Hade anatsatana naye; ndipo anawapatsa ulamuliro pa dera lacinai la dziko, kukapha ndi lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndi zirombo za padziko.


Revelation 9:6
Ndipo m'masiku ajawo, anthu adzafunafuna imfa osaipeza konse; ndipo adzakhumba kumwalira, koma imfa idzawathawa.


Revelation 12:11
Ndipo iwo anamlaka iye cifukwa ca mwazi wa Mwanawankhosa, ndi cifukwa ca mau a umboni wao; ndipo sanakonda moyo wao kungakhale kufikira imfa.


Revelation 13:3
Ndipo umodzi wa mitu yace unakhala ngati unalasidwa kufikira imfa; ndipo bala lace la kuimfa lidapola; ndipo dziko lonse linazizwa potsata ciromboco;


Revelation 13:12
Ndipo cicita ulamuliro wonse wa cirombo coyamba pamaso pace. Ndipo cilambiritsa dziko ndi iwo akukhala momwemo cirombo coyamba, cimene bala lace la kuimfa lidapola.


Revelation 18:8
Cifukwa cace miliri yace idzadzam'tsiku limodzi, imfa, ndi maliro, ndi njala; ndipo udzapserera ndi moto; cifukwa Ambuye Mulungu wouweruza ndiye wolimba.


Revelation 20:6
Wodala ndi woyera mtima ali iye amene acita nao pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yaciwiri iribe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzacita ufumu pamodzi ndi iye zaka cikwizo.


Revelation 20:13
Ndipo nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufawo anali m'menemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa nchito zace,


Revelation 20:14
Ndipo imfa ndi Hade zinaponyedwa m'nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yaciwiri, ndiyo nyanja yamoto.


Revelation 21:4
ndipo adzawapukutira misozi yonse kuicotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena cowawitsa; zoyambazo zapita.


Revelation 21:8
Koma amantha, ndi osakhulupira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi acigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, colandira cao cidzakhala m'nyanja yotentha ndi mota ndi sulfure; ndiyo imfa yaciwiri.


English Amplified Bible
Copyright © 2015 by The Lockman Foundation, La Habra, CA 90631. All rights reserved.