1 |
Pa tsiku loyamba la Sabata, mmamawa kwambiri, amayi anatenga zonunkhira napita ku manda. |
2 |
Anaona mwala wa pa manda utagubuduzika |
3 |
ndipo atalowamo sanapeze mtembo wa Ambuye Yesu. |
4 |
Pamene iwo ankadabwa za zimenezi, mwadzidzidzi, amuna awiri ovala zovala zonyezimira kwambiri anayimirira pambali pawo. |
5 |
Ndi mantha, amayiwo anaweramitsa nkhope zawo pansi, koma amunawo anawawuza kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukufuna wamoyo pakati pa akufa? |
6 |
Iye sali muno ayi. Wauka! Kumbukirani zimene anakuwuzani pamene anali nanu ku Galileya: |
7 |
‘Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa, napachikidwa ndipo tsiku lachitatu adzaukitsidwanso.’ ” |
8 |
Ndipo anakumbukira mawu ake. |
9 |
Atabwerera kuchokera ku mandako, anafotokoza zinthu zonse kwa khumi ndi mmodziwo ndi kwa ena onse. |
10 |
Amayi anali Mariya Magadalena, Yohana, Mariya amayi a Yakobo, ndi ena anali nawo amene anawuza atumwi. |
11 |
Koma iwo sanawakhulupirire amayiwa, chifukwa mawu awo amaoneka kwa iwo ngati opanda nzeru. |
12 |
Komabe Petro anayimirira ndi kuthamangira ku manda. Atasuzumira, anaona nsalu zimene anamukulungira zija zili pa zokha, ndipo iye anachoka, akudabwa ndi zimene zinachitikazo. |
13 |
Ndipo tsiku lomwelo, awiri a iwo ankapita ku mudzi wotchedwa Emau, pafupifupi makilomita khumi ndi imodzi kuchokera ku Yerusalemu. |
14 |
Iwo ankayankhulana za zonse zimene zinachitikazo. |
15 |
Pamenepo Yesu mwini wake anabwera ndi kuyenda nawo pamodzi; |
16 |
koma iwo sanamuzindikire. |
17 |
Iye anawafunsa kuti, “Kodi mukukambirana zotani mʼnjira muno?” Iwo anayima ndi nkhope zakugwa. |
18 |
Mmodzi wa iwo wotchedwa Kaliyopa anamufunsa kuti, “Kodi ndiwe wekha wokhala mu Yerusalemu amene sukudziwa zinthu zimene zachitika mʼmasiku awa?” |
19 |
Iye anafunsa kuti, “Zinthu zotani?” Iwo anayankha nati, “Za Yesu wa ku Nazareti, Iye anali mneneri, wamphamvu mʼmawu ndi mu zochita pamaso pa Mulungu ndi anthu onse. |
20 |
Akulu a ansembe ndi oweruza anamupereka Iye kuti aphedwe, ndipo anamupachika Iye; |
21 |
koma ife tinkayembekezera kuti Iye ndiye amene akanawombola Israeli. Ndipo kuwonjeza apo, lero ndi tsiku lachitatu chichitikireni izi. |
22 |
Kuwonjezanso apo, ena mwa amayi athu atidabwitsa ife. Iwo anapita ku manda mmamawa |
23 |
koma sanakapeze mtembo wake. Iwo anabwera ndi kudzatiwuza ife kuti anaona masomphenya a angelo amene anati Yesu ali moyo. |
24 |
Kenaka ena mwa anzathu anapita ku manda ndipo anakapeza monga momwe amayiwo ananenera, koma Iye sanamuone.” |
25 |
Iye anawawuza kuti, “Inu ndinu anthu opusa, osafuna kukhulupirira msanga zonse zimene aneneri ananena! |
26 |
Kodi Khristu sanayenera kumva zowawa izi ndipo kenaka ndi kulowa mu ulemerero wake?” |
27 |
Ndipo kuyambira ndi Mose ndi aneneri onse Iye anawafotokozera zimene zinalembedwa mʼmalemba wonse zokhudzana ndi Iye mwini. |
28 |
Atayandikira mudzi omwe amapitako, Yesu anachita ngati akupitirira. |
29 |
Koma iwo anamupempha Iye kwambiri kuti, “Mukhale ndi ife, popeza kwatsala pangʼono kuda, ndipo dzuwa lili pafupi kulowa.” Ndipo Iye anapita kukakhala nawo. |
30 |
Iye ali pa tebulo pamodzi nawo, anatenga buledi ndipo anayamika, nanyema nayamba kuwagawira. |
31 |
Kenaka maso awo anatsekuka ndipo anamuzindikira Iye, ndipo anachoka pakati pawo. |
32 |
Iwo anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi mitima yathu sinali kutentha mʼkati mwathu pamene Iye ankayankhulana nafe pa njira ndi mmene anatitsekulira malemba?” |
33 |
Nthawi yomweyo iwo anayimirira ndi kubwerera ku Yerusalemu. Iwo anapeza khumi ndi mmodziwo ndi ena anali nawo nasonkhana pamodzi |
34 |
ndipo anati, “Ndi zoonadi! Ambuye auka ndipo anaonekera kwa Simoni.” |
35 |
Kenaka awiriwo anawawuza zimene zinachitika pa njira, ndi mmene iwo anamudziwira Yesu, Iye atanyema buledi. |
36 |
Akufotokoza zimenezi, Yesu mwini wake anayimirira pakati pawo ndipo anati, “Mukhale ndi mtendere.” |
37 |
Koma chifukwa choti anathedwa nzeru ndi kuchita mantha, ankaganiza kuti akuona mzukwa. |
38 |
Iye anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukuvutika? Nʼchifukwa chiyani mukukayika mu mtima mwanu? |
39 |
Taonani manja anga ndi mapazi anga. Ine ndine amene! Khudzeni kuti muone. Mzukwa ulibe mnofu ndi mafupa monga mukuonera ndili nazo.” |
40 |
Iye atanena izi anawaonetsa manja ake ndi mapazi ake. |
41 |
Ndipo pamene iwo samakhulupirirabe, chifukwa cha chimwemwe ndi kudabwa, Iye anawafunsa kuti, “Kodi muli ndi chakudya chilichonse pano?” |
42 |
Iwo anamupatsa Iye kachidutswa ka nsomba yophika. |
43 |
Iye anakatenga ndi kukadya iwo akuona. |
44 |
Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene ndinakuwuzani pamene ndinali nanu: chilichonse chiyenera kukwaniritsidwa chimene chinalembedwa cha Ine mʼbuku la Malamulo a Mose, Aneneri ndi Masalimo.” |
45 |
Kenaka anawatsekula maganizo kuti azindikire Malemba. |
46 |
Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene zinalembedwa: Khristu adzazunzika ndipo adzauka kwa akufa tsiku lachitatu. |
47 |
Ndipo kutembenuka mtima ndi kukhululukidwa kwa machimo zidzalalikidwa mu dzina lake kwa anthu amitundu yonse kuyambira mu Yerusalemu. |
48 |
Inu ndinu mboni za zimenezi. |
49 |
Ine ndidzakutumizirani chimene Atate anga analonjeza. Koma khalani mu mzinda muno mpaka mutavekedwa mphamvu yochokera kumwamba.” |
50 |
Iye atawatengera kunja kwa mzindawo mpaka ku Betaniya, anakweza manja ake ndi kuwadalitsa. |
51 |
Iye akuwadalitsa, anawasiya ndipo anatengedwa kupita kumwamba. |
52 |
Pamenepo anamulambira Iye ndipo anabwerera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu. |
53 |
Ndipo iwo anakhalabe ku Nyumba ya Mulungu, akulemekeza Mulungu.
|
Chewa Bible 2016 |
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® |
|
|
|
|
|
|
|
|
|
|
LUKA 24:1 |
LUKA 24:2 |
LUKA 24:3 |
LUKA 24:4 |
LUKA 24:5 |
LUKA 24:6 |
LUKA 24:7 |
LUKA 24:8 |
LUKA 24:9 |
LUKA 24:10 |
LUKA 24:11 |
LUKA 24:12 |
LUKA 24:13 |
LUKA 24:14 |
LUKA 24:15 |
LUKA 24:16 |
LUKA 24:17 |
LUKA 24:18 |
LUKA 24:19 |
LUKA 24:20 |
LUKA 24:21 |
LUKA 24:22 |
LUKA 24:23 |
LUKA 24:24 |
LUKA 24:25 |
LUKA 24:26 |
LUKA 24:27 |
LUKA 24:28 |
LUKA 24:29 |
LUKA 24:30 |
LUKA 24:31 |
LUKA 24:32 |
LUKA 24:33 |
LUKA 24:34 |
LUKA 24:35 |
LUKA 24:36 |
LUKA 24:37 |
LUKA 24:38 |
LUKA 24:39 |
LUKA 24:40 |
LUKA 24:41 |
LUKA 24:42 |
LUKA 24:43 |
LUKA 24:44 |
LUKA 24:45 |
LUKA 24:46 |
LUKA 24:47 |
LUKA 24:48 |
LUKA 24:49 |
LUKA 24:50 |
LUKA 24:51 |
LUKA 24:52 |
LUKA 24:53 |
|
|
|
|
|
|
LUKA 1 / LUK 1 |
LUKA 2 / LUK 2 |
LUKA 3 / LUK 3 |
LUKA 4 / LUK 4 |
LUKA 5 / LUK 5 |
LUKA 6 / LUK 6 |
LUKA 7 / LUK 7 |
LUKA 8 / LUK 8 |
LUKA 9 / LUK 9 |
LUKA 10 / LUK 10 |
LUKA 11 / LUK 11 |
LUKA 12 / LUK 12 |
LUKA 13 / LUK 13 |
LUKA 14 / LUK 14 |
LUKA 15 / LUK 15 |
LUKA 16 / LUK 16 |
LUKA 17 / LUK 17 |
LUKA 18 / LUK 18 |
LUKA 19 / LUK 19 |
LUKA 20 / LUK 20 |
LUKA 21 / LUK 21 |
LUKA 22 / LUK 22 |
LUKA 23 / LUK 23 |
LUKA 24 / LUK 24 |