A A A A A
Facebook Instagram Twitter
Chewa Bible 2014

AKOLOSE 41
Ambuye inu, chitirani akapolo anu cholungama ndi cholingana; podziwa kuti inunso muli naye Mbuye m'Mwamba.
2
Chitani khama m'kupemphera, nimudikire momwemo ndi chiyamiko;
3
ndi kutipempherera ifenso pomwepo, kuti Mulungu atitsegulire ife pakhomo pa mau, kuti tilankhule chinsinsi cha Khristu; chimenenso ndikhalira m'ndende,
4
kuti ndichionetse ichi monga ndiyenera kulankhula.
5
Muyendere munzeru ndi iwo akunja, kuchita machawi nthawi ingatayike.
6
Mau anu akhale m'chisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.
7
Zonse za kwa ine adzakuzindikiritsani Tikiko, mbale wokondedwa ndi mtumiki wokhulupirika ndi kapolo mnzanga mwa Ambuye:
8
amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichi chomwe, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti atonthoze mitima yanu;
9
pamodzi ndi Onesimo, mbale wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ali wa kwa inu. Zonse za kuno adzakuzindikiritsani inu.
10
Aristariko wam'ndende mnzanga akupatsani moni, ndi Marko, msuweni wa Barnabasi (amene munalandira zolamulira za kwa iye; akafika kwanu, mumlandire iye),
11
ndi Yesu, wotchedwa Yusto, ndiwo a mdulidwe; iwo okha ndiwo antchito anzanga a mu Ufumu wa Mulungu, ndiwo akundikhalira ine chonditonthoza mtima.
12
Akupatsani moni Epafra ndiye wa kwa inu, ndiye kapolo wa Khristu Yesu, wakulimbira chifukwa cha inu m'mapemphero ake masiku onse, kuti mukaime amphumphu ndi odzazidwa m'chifuniro chonse cha Mulungu.
13
Pakuti ndimchitira iye umboni kuti adziwawitsa nayo ntchito chifukwa cha inu, ndi iwo a m'Laodikea, ndi iwo a m'Hierapoli.
14
Akupatsani moni Luka sing'anga wokondedwa, ndi Dema.
15
Akupatsani moni abalewo a m'Laodikea, ndi Nimfa, ndi Mpingowo wa m'nyumba yao.
16
Ndipo pamene mudamwerenga kalata uyu, amwerengenso mu Mpingo wa ku Laodikea, ndi inunso muwerenge wa ku Laodikea.
17
Ndipo nenani kwa Arkipo, Samaliratu utumiki umene udaulandira mwa Ambuye, kuti uukwanitse.
18
Ndipereka moni ndi dzanja langa, kwa ine Paulo. Kumbukirani zomangira zanga. Chisomo chikhale nanu.AKOLOSE 4:1
AKOLOSE 4:2
AKOLOSE 4:3
AKOLOSE 4:4
AKOLOSE 4:5
AKOLOSE 4:6
AKOLOSE 4:7
AKOLOSE 4:8
AKOLOSE 4:9
AKOLOSE 4:10
AKOLOSE 4:11
AKOLOSE 4:12
AKOLOSE 4:13
AKOLOSE 4:14
AKOLOSE 4:15
AKOLOSE 4:16
AKOLOSE 4:17
AKOLOSE 4:18


AKOLOSE 1 / AKO 1
AKOLOSE 2 / AKO 2
AKOLOSE 3 / AKO 3
AKOLOSE 4 / AKO 4