A A A A A
Facebook Instagram Twitter
Chewa Bible 2014

AROMA 161
Ndipereka kwa inu Febe, mlongo wathu, ndiye mtumiki wamkazi wa Mpingo wa Ambuye wa ku Kenkrea;
2
kuti mumlandire iye mwa Ambuye, monga kuyenera oyera mtima, ndi kuti mumthandize m'zinthu zilizonse adzazifuna kwa inu; pakuti iye yekha anali wosungira ambiri, ndi ine ndemwe.
3
Mupereke moni kwa Prisika ndi Akwila, antchito anzanga mwa Khristu Yesu,
4
amene anapereka khosi lao chifukwa cha moyo wanga; amene ndiwayamika, si ine ndekha, komanso Mipingo yonse ya Ambuye ya kwa anthu amitundu;
5
ndipo mupereke moni kwa Mpingo wa Ambuye wa m'nyumba mwao. Moni kwa Epeneto wokondedwa wanga, ndiye chipatso choundukula cha Asiya cha kwa Khristu.
6
Moni kwa Maria amene anadzilemetsa ndi ntchito zambiri zothandiza inu.
7
Moni kwa Androniko ndi Yunia, anansi anga, ndi andende anzanga, amene ali omveka mwa atumwi, amenenso ananditsogolera ine mwa Khristu.
8
Moni kwa Ampiliato wokondedwa wanga mwa Ambuye.
9
Moni kwa Urbano wantchito mnzathu mwa Khristu, ndi Stakisi wokondedwa wanga.
10
Moni kwa Apelesi, wovomerezedwayo mwa Khristu. Moni iwo a kwa Aristobulo.
11
Moni kwa Herodiono, mbale wanga. Moni iwo a kwa Narkiso, amene ali mwa Ambuye.
12
Moni kwa Trifena, ndi Trifosa amene agwiritsa ntchito mwa Ambuye. Moni kwa Perisi, wokondedwayo amene anagwiritsa ntchito zambiri mwa Ambuye.
13
Moni kwa Rufu, wosankhidwayo mwa Ambuye, ndi amai wake ndi wanga.
14
Moni kwa Asinkrito, Filegoni, Heremesi, Patrobasi, Herimasi ndi abale amene ali nao.
15
Moni Filologo ndi Juliya, Nereo ndi mlongo wake, ndi Olimpasi, ndi oyera mtima onse ali pamodzi nao.
16
Mupatsane moni wina ndi mnzake ndi kupsompsona kupatulika. Mipingo yonse ya Khristu ikupatsani moni.
17
Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang'anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zophunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo.
18
Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Khristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa.
19
Pakuti kumvera kwanu kunabuka kwa anthu onse. Chifukwa chake ndikondwera ndi inu; koma ndifuna kuti mukakhale anzeru pa zabwino, koma ozungulidwa pa zoipa.
20
Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.
21
Timoteo wantchito mnzanga akupatsani moni; ndi Lusio ndi Yasoni ndi Sosipatere, abale anga.
22
Ine Tersio, ndilikulemba kalata ameneyu, ndikupereka moni mwa Ambuye.
23
Gayo, mwini nyumba wolandira ine, ndi Mpingo wonse wa Ambuye, akupereka moni. Erasto, ndiye woyang'anira mudzi, akupereka moni, ndiponso Kwarto mbaleyo.
24
***
25
Ndipo kwa Iye amene ali wamphamvu yakukhazikitsa inu monga mwa Uthenga wanga Wabwino, ndi kulalikira kwa Yesu Khristu, monga mwa vumbulutso la chinsinsi chimene chinabisika mwa nthawi zonse zosayamba,
26
koma chaonetsedwa tsopano, ndi kudziwidwa kwa anthu a mitundu yonse mwa malembo a aneneriwo, monga mwa lamulo la Mulungu wosatha, kuti amvere chikhulupiriro;
27
kwa Mulungu wanzeru yekhayo, mwa Yesu Khristu, kwa yemweyo ukhale ulemerero kunthawi zonse. Amen.AROMA 16:1
AROMA 16:2
AROMA 16:3
AROMA 16:4
AROMA 16:5
AROMA 16:6
AROMA 16:7
AROMA 16:8
AROMA 16:9
AROMA 16:10
AROMA 16:11
AROMA 16:12
AROMA 16:13
AROMA 16:14
AROMA 16:15
AROMA 16:16
AROMA 16:17
AROMA 16:18
AROMA 16:19
AROMA 16:20
AROMA 16:21
AROMA 16:22
AROMA 16:23
AROMA 16:24
AROMA 16:25
AROMA 16:26
AROMA 16:27


AROMA 1 / ARO 1
AROMA 2 / ARO 2
AROMA 3 / ARO 3
AROMA 4 / ARO 4
AROMA 5 / ARO 5
AROMA 6 / ARO 6
AROMA 7 / ARO 7
AROMA 8 / ARO 8
AROMA 9 / ARO 9
AROMA 10 / ARO 10
AROMA 11 / ARO 11
AROMA 12 / ARO 12
AROMA 13 / ARO 13
AROMA 14 / ARO 14
AROMA 15 / ARO 15
AROMA 16 / ARO 16