A A A A A
Facebook Instagram Twitter
Chewa Bible 2014

CHIVUMBULUTSO 81
Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachisanu ndi chiwiri, munali chete m'Mwamba monga mwa nthawi ya ora latheka.
2
Ndipo ndinaona angelo asanu ndi awiri amene amaimirira pamaso pa Mulungu; ndipo anawapatsa malipenga asanu ndi awiri.
3
Ndipo anadza mngelo wina, naima pa guwa la nsembe, nakhala nacho chotengera cha zofukiza chagolide; ndipo anampatsa zofukiza zambiri, kuti aziike pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima onse pa guwa la nsembe lagolide, lokhala kumpando wachifumu.
4
Ndipo utsi wa zofukiza, pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima unakwera kutuluka m'dzanja la mngelo, pamaso pa Mulungu.
5
Ndipo mngeloyo anatenga mbale ya zofukiza, naidzaza ndi moto wopala pa guwa la nsembe, nauponya pa dziko lapansi; ndipo panakhala mabingu, ndi mau, ndi mphezi, ndi chivomezi.
6
Ndipo angelo asanu ndi awiri akukhala nao malipenga anadzikonzera kuti aombe.
7
Ndipo woyamba anaomba lipenga, ndipo panakhala matalala ndi moto, zosanganiza ndi mwazi, ndipo anazitaya pa dziko lapansi; ndipo limodzi la magawo atatu a dziko lidapserera, ndipo limodzi la magawo atatu a mitengo lidapserera, ndipo msipu wonse udapserera.
8
Ndipo mngelo wachiwiri anaomba lipenga, ndipo monga ngati phiri lalikulu lakupserera ndi moto linaponyedwa m'nyanja; ndipo limodzi la magawo atatu a nyanja linasanduka mwazi;
9
ndipo lidafa limodzi la magawo atatu a zolengedwa zili m'nyanja, zokhala ndi moyo; ndipo limodzi la magawo atatu a zombo lidaonongeka.
10
Ndipo mngelo wachitatu anaomba lipenga, ndipo idagwa kuchokera kumwamba nyenyezi yaikulu, yoyaka ngati muuni, ndipo idagwa pa limodzi la magawo atatu a mitsinje, ndi pa akasupe amadzi;
11
ndipo dzina lake la nyenyeziwo alitcha Chowawa; ndipo limodzi la magawo atatu a madzi lidasanduka chowawa; ndipo anthu ambiri adafa pakumwa madzi, pakuti asananduka owawa.
12
Ndipo mngelo wachinai anaomba lipenga, ndipo limodzi la magawo atatu a dzuwa linagwidwa, ndi limodzi la magawo atatu a mwezi, ndi limodzi la magawo atatu a nyenyezi; kuti limodzi la magawo ao atatu lidetsedwe, ndi kuti limodzi la magawo ake atatu a usana lisawale, ndi usiku momwemo.
13
Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva chiombankhanga chilikuuluka pakati pa mwamba, ndi kunena ndi mau akulu, Tsoka, tsoka, tsoka, iwo akukhala padziko, chifukwa cha mau otsala a lipenga la angelo atatu asanaombe.CHIVUMBULUTSO 8:1
CHIVUMBULUTSO 8:2
CHIVUMBULUTSO 8:3
CHIVUMBULUTSO 8:4
CHIVUMBULUTSO 8:5
CHIVUMBULUTSO 8:6
CHIVUMBULUTSO 8:7
CHIVUMBULUTSO 8:8
CHIVUMBULUTSO 8:9
CHIVUMBULUTSO 8:10
CHIVUMBULUTSO 8:11
CHIVUMBULUTSO 8:12
CHIVUMBULUTSO 8:13


CHIVUMBULUTSO 1 / CHI 1
CHIVUMBULUTSO 2 / CHI 2
CHIVUMBULUTSO 3 / CHI 3
CHIVUMBULUTSO 4 / CHI 4
CHIVUMBULUTSO 5 / CHI 5
CHIVUMBULUTSO 6 / CHI 6
CHIVUMBULUTSO 7 / CHI 7
CHIVUMBULUTSO 8 / CHI 8
CHIVUMBULUTSO 9 / CHI 9
CHIVUMBULUTSO 10 / CHI 10
CHIVUMBULUTSO 11 / CHI 11
CHIVUMBULUTSO 12 / CHI 12
CHIVUMBULUTSO 13 / CHI 13
CHIVUMBULUTSO 14 / CHI 14
CHIVUMBULUTSO 15 / CHI 15
CHIVUMBULUTSO 16 / CHI 16
CHIVUMBULUTSO 17 / CHI 17
CHIVUMBULUTSO 18 / CHI 18
CHIVUMBULUTSO 19 / CHI 19
CHIVUMBULUTSO 20 / CHI 20
CHIVUMBULUTSO 21 / CHI 21
CHIVUMBULUTSO 22 / CHI 22