1 |
Paulo, wandende wa Khristu Yesu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Filemoni wokondedwayo ndi wantchito mnzathu, |
2 |
ndi kwa Afiya mlongoyo, ndi Arkipo msilikali mnzathu, ndi kwa Mpingo uli m'nyumba yako: |
3 |
Chisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu. |
4 |
Ndiyamika Mulungu wanga nthawi zonse, ndi kukumbukira iwe m'mapemphero anga, |
5 |
pakumva za chikondi chako ndi chikhulupiriro uli nacho chakulinga kwa Ambuye Yesu, ndi kwa oyera mtima onse; |
6 |
kuti chiyanjano cha chikhulupiriro chako chikakhale champhamvu podziwa chabwino chilichonse chili mwa inu, cha kwa Khristu. |
7 |
Pakuti ndinali nacho chimwemwe chambiri ndi chisangalatso pa chikondi chako, popeza mitima ya oyera mtima yatsitsimuka mwa iwe, mbale. |
8 |
Momwemo, ndingakhale ndili nako kulimbika mtima kwakukulu m'Khristu kukulamulira chimene chiyenera, |
9 |
koma makamaka ndidandaulira mwa chikondi, pokhala wotere, Paulo nkhalamba, ndipo tsopano wandendenso wa Khristu Yesu; |
10 |
ndikudandaulira chifukwa cha mwana wanga, amene ndambala m'ndende, Onesimo, |
11 |
amene kale sanakupindulira, koma tsopano watipindulira bwino iwe ndi ine; |
12 |
amene ndi yemweyo ndakubwezera iwe, ndiye mtima weniweni wa ine. |
13 |
Ameneyo ndikadafuna ine kumsunga akhale nane, kuti m'malo mwako akadanditumikira ine m'ndende za Uthenga Wabwino: |
14 |
koma wopanda kudziwa mtima wako sindinafuna kuchita kanthu; kuti ubwino wako usakhale monga mokakamiza, komatu mwaufulu. |
15 |
Pakuti kapena anasiyanitsidwa ndi iwe kanthawi chifukwa cha ichi, ndi kuti udzakhala naye nthawi zonse; |
16 |
osatinso monga kapolo, koma woposa kapolo, mbale wokondedwa, makamaka ndi ine, koma koposa nanga ndi iwe, m'thupi, ndiponso mwa Ambuye. |
17 |
Ngati tsono undiyesa woyanjana nawe, umlandire iye monga ine mwini. |
18 |
Koma ngati anakulakwira kanthu, kapena wokongola kanthu, kanthu, kapena wakongola kanthu, undiwerengere ine kameneko; |
19 |
ine Paulo ndichilemba ndi dzanja langa, ndidzachibwezera ine; kuti ndisanene nawe kuti iwe ndiwe mangawa anga. |
20 |
Inde, mbale, ndikondwere nawe mwa Ambuye: utsitsimutse mtima wanga mwa Khristu. |
21 |
Pokhulupirira kumvera kwako ndikulembera iwe, podziwa kuti udzachitanso koposa chimene ndinena. |
22 |
Koma undikonzerenso pogona; pakuti ndiyembekeza kuti mwa mapemphero anu ndidzapatsidwa kwa inu. |
23 |
Epafra wandende mnzanga mwa Khristu Yesu akukupatsa moni; |
24 |
ateronso, Marko, Aristariko, Dema, Luka, antchito anzanga. |
25 |
Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale pamodzi ndi mzimu wanu. Amen.
|
Chewa Bible 2014 |
Bible Society of Malawi |
|
|
|
|
|
|
|
|
|
|
FILEMONI 1:1 |
FILEMONI 1:2 |
FILEMONI 1:3 |
FILEMONI 1:4 |
FILEMONI 1:5 |
FILEMONI 1:6 |
FILEMONI 1:7 |
FILEMONI 1:8 |
FILEMONI 1:9 |
FILEMONI 1:10 |
FILEMONI 1:11 |
FILEMONI 1:12 |
FILEMONI 1:13 |
FILEMONI 1:14 |
FILEMONI 1:15 |
FILEMONI 1:16 |
FILEMONI 1:17 |
FILEMONI 1:18 |
FILEMONI 1:19 |
FILEMONI 1:20 |
FILEMONI 1:21 |
FILEMONI 1:22 |
FILEMONI 1:23 |
FILEMONI 1:24 |
FILEMONI 1:25 |
|
|
|
|
|
|
FILEMONI 1 / FIL 1 |