A A A A A
Facebook Instagram Twitter
Chewa Bible 2014

1 ATESALONIKA 51
Koma za nthawizo ndi nyengozo, abale, sikufunika kuti tidzakulemberani.
2
Pakuti inu nokha mudziwa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku.
3
Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chionongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.
4
Koma inu, abale, simuli mumdima, kuti tsikulo likakugwereni monga mbala;
5
pakuti inu nonse muli ana a kuunika, ndi ana a usana; sitili a usiku, kapena a mdima;
6
chifukwa chake tsono tisagone monga otsalawo, komatu tidikire, ndipo tisaledzere.
7
Pakuti iwo akugona agona usiku; ndi iwo akuledzera aledzera usiku.
8
Koma ife popeza tili a usana tisaledzere, titavala chapachifuwa cha chikhulupiriro ndi chikondi; ndi chisoti chili chiyembekezo cha chipulumutso.
9
Pakuti Mulungu sanatiika ife tilawe mkwiyo, komatu kuti tilandire chipulumutso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu,
10
amene anafa m'malo mwathu, kuti, tingakhale tidikira, tingakhale tigona, tikakhale ndi moyo pamodzi ndi Iye.
11
Mwa ichi chenjezanani, ndipo mangiriranani wina ndi mnzake, monganso mumachita.
12
Koma, abale, tikupemphani, dziwani iwo akugwiritsa ntchito mwa inu, nakhala akulu anu mwa Ambuye, nakuyambirirani inu;
13
ndipo muwachitire ulemu woposatu mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yao. Khalani mumtendere mwa inu nokha.
14
Koma tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi, limbikitsani amantha mtima? Chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.
15
Penyani kuti wina asabwezere choipa womchitira choipa; komatu nthawi zonse mutsatire chokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse.
16
Kondwerani nthawi zonse;
17
Pempherani kosaleka;
18
M'zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu.
19
Musazime Mzimuyo;
20
Musanyoze manenero;
21
Yesani zonse; sungani chokomacho,
22
Mupewe maonekedwe onse a choipa.
23
Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda chilema pa kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
24
Wakuitana inu ali wokhulupirika, amenenso adzachichita.
25
Abale, tipempherereni ife.
26
Perekani moni kwa abale onse ndi chipsompsono chopatulika.
27
Ndikulumbirirani pa Ambuye kuti kalatayu awerengedwe kwa abale onse.
28
Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale nanu.1 ATESALONIKA 5:1
1 ATESALONIKA 5:2
1 ATESALONIKA 5:3
1 ATESALONIKA 5:4
1 ATESALONIKA 5:5
1 ATESALONIKA 5:6
1 ATESALONIKA 5:7
1 ATESALONIKA 5:8
1 ATESALONIKA 5:9
1 ATESALONIKA 5:10
1 ATESALONIKA 5:11
1 ATESALONIKA 5:12
1 ATESALONIKA 5:13
1 ATESALONIKA 5:14
1 ATESALONIKA 5:15
1 ATESALONIKA 5:16
1 ATESALONIKA 5:17
1 ATESALONIKA 5:18
1 ATESALONIKA 5:19
1 ATESALONIKA 5:20
1 ATESALONIKA 5:21
1 ATESALONIKA 5:22
1 ATESALONIKA 5:23
1 ATESALONIKA 5:24
1 ATESALONIKA 5:25
1 ATESALONIKA 5:26
1 ATESALONIKA 5:27
1 ATESALONIKA 5:28


1 ATESALONIKA 1 / 1ATE 1
1 ATESALONIKA 2 / 1ATE 2
1 ATESALONIKA 3 / 1ATE 3
1 ATESALONIKA 4 / 1ATE 4
1 ATESALONIKA 5 / 1ATE 5