A A A A A
Facebook Instagram Twitter
Chewa Bible 2014

YOHANE 201
Koma tsiku loyamba la Sabata anadza Maria wa Magadala mamawa, kusanayambe kucha, kumanda, napenya mwala wochotsedwa kumanda.
2
Pomwepo anathamanga nadza kwa Simoni Petro ndi kwa wophunzira wina amene Yesu anamkonda, nanena nao, Anachotsa Ambuye kumanda, ndipo sitidziwa kumene anamuika Iye.
3
Anatuluka tsono Petro ndi wophunzira winayo, nalinkupita kumanda.
4
Koma anathamanga onse awiri pamodzi; ndipo wophunzira winayo anathamanga naposa Petro, nayamba kufika kumanda;
5
ndipo m'mene anawerama chosuzumira anaona nsalu zabafuta zitakhala, komatu sanalowamo.
6
Pamenepo anadzanso Simoni Petro alikumtsata iye, nalowa m'manda; ndipo anaona nsalu zabafuta zitakhala,
7
ndi mlezo, umene unali pamutu pake, wosakhala pamodzi ndi nsalu zabafuta, koma wopindika padera pamalo pena.
8
Pamenepo tsono analowanso wophunzira winayo, amene anayamba kufika kumanda, ndipo anaona, nakhulupirira.
9
Pakuti kufikira pomwepo sanadziwa lembo lakuti ayenera Iye kuuka kwa akufa.
10
Chifukwa chake ophunzirawo anachokanso, kunka kwao.
11
Koma Maria analikuima kumanda kunja, alikulira. Ndipo m'mene alikulira anawerama chisuzumirire kumanda;
12
ndipo anaona angelo awiri atavala zoyera, alikukhala mmodzi kumutu, ndi wina kumiyendo, kumene mtembo wa Yesu udagona.
13
Ndipo iwowa ananena kwa iye, Mkazi, uliranji? Ananena nao, Chifukwa anachotsa Ambuye wanga, ndipo sindidziwa kumene anamuika Iye.
14
M'mene adanena izi, anacheuka m'mbuyo, naona Yesu ali chilili, ndipo sanadziwa kuti ndiye Yesu.
15
Yesu ananena naye, Mkazi, uliranji? Ufuna yani? Iyeyu poyesa kuti ndiye wakumunda, ananena ndi Iye, Mbuye ngati mwamnyamula Iye, ndiuzeni kumene mwamuika Iye, ndipo ndidzamchotsa.
16
Yesu ananena naye, Maria. Iyeyu m'mene anacheuka, ananena ndi Iye m'Chihebri, Raboni; chimene chinenedwa, Mphunzitsi.
17
Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sinditha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Mulungu wanu.
18
Maria wa Magadala anapita, nalalikira kwa ophunzirawo, kuti, Ndaona Ambuye; ndi kuti ananena izi kwa iye.
19
Pamenepo, pokhala madzulo, tsiku lomwelo, loyamba la Sabata, makomo ali chitsekere, kumene anakhala ophunzira, chifukwa cha kuopa Ayuda, Yesu anadza naimirira pakati pao, nanena nao, Mtendere ukhale ndi inu.
20
Ndipo pamene adanena ichi, anaonetsa iwo manja ake ndi nthiti zake. Pamenepo ophunzira anakondwera pakuona Ambuye.
21
Chifukwa chake Yesu anatinso kwa iwo, Mtendere ukhale ndi inu; monga Atate wandituma Ine, Inenso ndituma inu.
22
Ndipo pamene anati ichi anawapumira, nanena nao, Landirani Mzimu Woyera.
23
Zochimwa za anthu ali onse muwakhululukira, zikhululukidwa kwa iwo; za iwo amene muzigwiritsa, zagwiritsidwa.
24
Koma Tomasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, wotchedwa Didimo, sanakhala nao pamodzi, pamene Yesu anadza.
25
Chifukwa chake ophunzira ena ananena naye, Tamuona Ambuye. Koma iye anati kwa iwo, Ndikapanda kuona m'manja ake chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika chala changa m'chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika dzanja langa kunthiti yake; sindidzakhulupirira.
26
Ndipo pakupita masiku asanu ndi atatu ophunzira ake analinso m'nyumbamo, ndi Tomasi pamodzi nao. Yesu anadza, makomo ali chitsekere, naimirira pakati, nati, Mtendere ukhale ndi inu.
27
Pomwepo ananena kwa Tomasi, Bwera nacho chala chako kuno, nuone manja anga, ndipo bwera nalo dzanja lako, nuliike kunthiti yanga, ndipo usakhale wosakhulupirira, koma wokhulupirira.
28
Tomasi anayankha nati kwa Iye, Ambuye wanga, ndi Mulungu wanga.
29
Yesu ananena kwa iye, Chifukwa wandiona Ine, wakhulupirira; odala iwo akukhulupirira, angakhale sanaona.
30
Ndipo zizindikiro zina zambiri Yesu anazichita pamaso pa ophunzira ake, zimene sizinalembedwa m'buku ili;
31
koma zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Khristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupirira mukhale nao moyo m'dzina lake.YOHANE 20:1
YOHANE 20:2
YOHANE 20:3
YOHANE 20:4
YOHANE 20:5
YOHANE 20:6
YOHANE 20:7
YOHANE 20:8
YOHANE 20:9
YOHANE 20:10
YOHANE 20:11
YOHANE 20:12
YOHANE 20:13
YOHANE 20:14
YOHANE 20:15
YOHANE 20:16
YOHANE 20:17
YOHANE 20:18
YOHANE 20:19
YOHANE 20:20
YOHANE 20:21
YOHANE 20:22
YOHANE 20:23
YOHANE 20:24
YOHANE 20:25
YOHANE 20:26
YOHANE 20:27
YOHANE 20:28
YOHANE 20:29
YOHANE 20:30
YOHANE 20:31


YOHANE 1 / YOH 1
YOHANE 2 / YOH 2
YOHANE 3 / YOH 3
YOHANE 4 / YOH 4
YOHANE 5 / YOH 5
YOHANE 6 / YOH 6
YOHANE 7 / YOH 7
YOHANE 8 / YOH 8
YOHANE 9 / YOH 9
YOHANE 10 / YOH 10
YOHANE 11 / YOH 11
YOHANE 12 / YOH 12
YOHANE 13 / YOH 13
YOHANE 14 / YOH 14
YOHANE 15 / YOH 15
YOHANE 16 / YOH 16
YOHANE 17 / YOH 17
YOHANE 18 / YOH 18
YOHANE 19 / YOH 19
YOHANE 20 / YOH 20
YOHANE 21 / YOH 21