A A A A A
×

Chewa Bible 2014

2 AKORINTO 11

1
Bwenzi mutandilola pang'ono ndi chopusacho! Komanso mundilole.
2
Pakuti ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya Mulungu; pakuti ndinakupalitsani ubwenzi mwamuna mmodzi, kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwa Khristu.
3
Koma ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Khristu.
4
Pakutitu ngati iye wakudza alalikira Yesu wina, amene ife sitinalalikira, kapena ngati mulandira mzimu wa mtundu wina, umene simunalandira, kapena Uthenga Wabwino wa mtundu wina umene simunalandira, mulolana naye bwino lomwe.
5
Pakuti ndiyesa kuti sindinaperewera konse ndi atumwi oposatu.
6
Ndipo ndingakhale ndili wosaphunzira m'manenedwe, koma sinditero m'chidziwitso, koma m'zonse tachionetsa kwa inu mwa anthu onse.
7
Kodi ndachimwa podzichepetsa ndekha, kuti inu mukakwezedwe, popeza ndinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu mwaufulu?
8
Ndinalanda za Mipingo ina, ndi kulandira kwa iwo kulipira kuti ndikatumikire inu;
9
ndipo pakukhala nanu, ndi kusowa, sindinasaukitsa munthu aliyense; pakuti abale akuchokera ku Masedoniya, anakwaniritsa kusowa kwanga; ndipo m'zonse ndinachenjera ndekha, ndisalemetse inu, ndipo ndidzachenjerapo.
10
Choonadi cha Khristu chili mwa ine, kuti kudzitamandira kumene sikudzaletsedwa kwa ine mu mbali za Akaya.
11
Chifukwa ninji? Chifukwa sindikonda inu kodi? Adziwa Mulungu.
12
Koma chimene ndichita, ndidzachitanso, kuti ndikawadulire chifukwa iwo akufuna chifukwa; kuti m'mene adzitamandiramo, apezedwe monganso ife.
13
Pakuti otere ali atumwi onyenga, ochita ochenjerera, odzionetsa ngati atumwi a Khristu.
14
Ndipo kulibe kudabwa; pakuti Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika.
15
Chifukwa chake sikuli kanthu kwakukulu ngatinso atumiki ake adzionetsa monga atumiki a chilungamo; amene chimaliziro chao chidzakhala monga ntchito zao.
16
Ndinenanso, Munthu asandiyese wopanda nzeru; koma ngati mutero, mundilandirenso ine monga wopanda nzeru, kuti inenso ndidzitamandire pang'ono.
17
Chimene ndilankhula sindilankhula monga mwa Ambuye, koma monga wopanda nzeru, m'kulimbika kumene kwa kudzitamandira.
18
Popeza ambiri adzitamandira monga mwa thupi, inenso ndidzadzitamandira.
19
Pakuti mulolana nao opanda nzeru mokondwera, pokhala anzeru inu nokha.
20
Pakuti mulola ngati wina akuyesani inu akapolo, ngati wina alikwira inu, ngati wina alanda zanu, ngati wina adzikuza, ngati wina akupandani pankhope.
21
Ndinena monga mwa kunyoza, monga ngati tinakhala ofooka. Koma m'mene wina alimbika mtimamo (ndinena mopanda nzeru) momwemo ndilimbika mtima inenso.
22
Kodi ali Ahebri? Inenso. Kodi ali Aisraele? Inenso. Kodi ali mbeu ya Abrahamu? Inenso.
23
Kodi ali atumiki a Khristu? (Ndilankhula monga moyaluka), makamaka ine; m'zivutinso mochulukira, m'ndende mochulukira, m'mikwingwirima mosawerengeka, muimfa kawirikawiri.
24
Kwa Ayuda ndinalandira kasanu mikwingwirima makumi anai kuperewera umodzi.
25
Katatu ndinamenyedwa ndi ndodo, kamodzi ndinaponyedwa miyala, katatu ndinatayika posweka chombo, ndinakhala m'kuya tsiku limodzi usana ndi usiku;
26
paulendo kawirikawiri, moopsa mwake mwa mitsinje, moopsa mwake mwa olanda, moopsa modzera kwa mtundu wanga, moopsa modzera kwa amitundu, moopsa m'mudzi, moopsa m'chipululu, moopsa m'nyanja, moopsa mwa abale onyenga;
27
m'chivutitso ndi m'cholemetsa, m'madikiro kawirikawiri, m'njala ndi ludzu, m'masalo a chakudya kawirikawiri, m'chisanu ndi umaliseche.
28
Popanda zakunjazo pali chondisindikiza tsiku ndi tsiku, chalabadiro cha Mipingo yonse.
29
Afooka ndani wosafooka inenso? Akhumudwitsidwa ndani, wosatenthanso ine?
30
Ngati ndiyenera kudzitamandira, ndidzadzitamandira ndi za kufooka kwanga.
31
Mulungu Atate wa Ambuye Yesu, Iye amene alemekezeka kunthawi yonse, adziwa kuti sindinama.
32
M'Damasiko kazembe wa mfumu Areta analindizitsa mudzi wa Adamasiko kuti andigwire ine;
33
ndipo mwa zenera, mudengu, ananditsitsa pakhoma, ndipo ndinapulumuka m'manja mwake.
2 AKORINTO 11:1
2 AKORINTO 11:2
2 AKORINTO 11:3
2 AKORINTO 11:4
2 AKORINTO 11:5
2 AKORINTO 11:6
2 AKORINTO 11:7
2 AKORINTO 11:8
2 AKORINTO 11:9
2 AKORINTO 11:10
2 AKORINTO 11:11
2 AKORINTO 11:12
2 AKORINTO 11:13
2 AKORINTO 11:14
2 AKORINTO 11:15
2 AKORINTO 11:16
2 AKORINTO 11:17
2 AKORINTO 11:18
2 AKORINTO 11:19
2 AKORINTO 11:20
2 AKORINTO 11:21
2 AKORINTO 11:22
2 AKORINTO 11:23
2 AKORINTO 11:24
2 AKORINTO 11:25
2 AKORINTO 11:26
2 AKORINTO 11:27
2 AKORINTO 11:28
2 AKORINTO 11:29
2 AKORINTO 11:30
2 AKORINTO 11:31
2 AKORINTO 11:32
2 AKORINTO 11:33
2 AKORINTO 1 / 2AK 1
2 AKORINTO 2 / 2AK 2
2 AKORINTO 3 / 2AK 3
2 AKORINTO 4 / 2AK 4
2 AKORINTO 5 / 2AK 5
2 AKORINTO 6 / 2AK 6
2 AKORINTO 7 / 2AK 7
2 AKORINTO 8 / 2AK 8
2 AKORINTO 9 / 2AK 9
2 AKORINTO 10 / 2AK 10
2 AKORINTO 11 / 2AK 11
2 AKORINTO 12 / 2AK 12
2 AKORINTO 13 / 2AK 13