A A A A A
×

Chewa Bible 2014

MATEYU 1

1
Buku la kubadwa kwa Yesu Khristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu.
2
Abrahamu anabala Isaki; ndi Isaki anabala Yakobo; ndi Yakobo anabala Yuda ndi abale ake;
3
ndi Yuda anabala Perezi ndi Zera mwa Tamara; ndi Perezi anabala Hezironi; ndi Hezironi anabala Ramu;
4
ndi Ramu anabala Aminadabu; ndi Aminadabu anabala Nasoni; ndi Nasoni anabala Salimoni;
5
ndi Salimoni anabala Bowazi mwa Rahabu; ndi Bowazi anabala Obede mwa Rute; ndi Obede anabala Yese;
6
ndi Yese anabala Davide mfumuyo. Ndipo Davide anabala Solomoni mwa mkazi wa Uriya;
7
ndi Solomoni anabala Rehobowamu; ndi Rehobowamu anabala Abiya; ndi Abiya anabala Asa;
8
ndi Asa anabala Yehosafati; ndi Yehosafati anabala Yoramu; ndi Yoramu anabala Uziya;
9
ndi Uziya anabala Yotamu; ndi Yotamu anabala Ahazi; ndi Ahazi anabala Hezekiya;
10
ndi Hezekiya anabala Manase; ndi Manase anabala Amoni; ndi Amoni anabala Yosiya;
11
ndi Yosiya anabala Yekoniya ndi abale ake pa nthawi yakutengedwa kunka ku Babiloni.
12
Ndipo pambuyo pake pa kutengedwako ku Babiloni, Yekoniya anabala Sealatiele; ndi Sealatiele anabala Zerubabele;
13
ndi Zerubabele anabala Abihudi; ndi Abihudi anabala Eliyakimu; ndi Eliyakimu anabala Azoro;
14
ndi Azoro anabala Zadoki; ndi Zadoki anabala Akimu; ndi Akimu anabala Eliudi;
15
ndi Eliudi anabala Eleazara; ndi Eleazara anabala Matani; ndi Matani anabala Yakobo;
16
ndi Yakobo anabala Yosefe, mwamuna wake wa Maria, amene Yesu, wotchedwa Khristu, anabadwa mwa iye.
17
Motero mibadwo yonse kuyambira pa Abrahamu kufikira kwa Davide ndiyo mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa Davide kufikira pa kutengedwa kunka ku Babiloni mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa kutengedwa kunka ku Babiloni kufikira kwa Khristu mibadwo khumi ndi inai.
18
Ndipo kubadwa kwake kwa Yesu Khristu kunali kotere: Amai wake Maria anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera.
19
Koma Yosefe, mwamuna wake, anali wolungama, ndiponso sanafune kunyazitsa iye, nayesa m'mtima kumleka iye m'tseri.
20
Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m'kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Maria mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chili cha Mzimu Woyera.
21
Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo ao.
22
Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndi kuti,
23
Onani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamutcha dzina lake, Imanuele. Ndilo losandulika, Mulungu nafe.
24
Ndipo Yosefe anauka tulo take, nachita monga anamuuza mngelo wa Ambuye, nadzitengera yekha mkazi wake;
25
ndipo sanamdziwe iye kufikira atabala mwana wake; namutcha dzina lake Yesu.
MATEYU 1:1
MATEYU 1:2
MATEYU 1:3
MATEYU 1:4
MATEYU 1:5
MATEYU 1:6
MATEYU 1:7
MATEYU 1:8
MATEYU 1:9
MATEYU 1:10
MATEYU 1:11
MATEYU 1:12
MATEYU 1:13
MATEYU 1:14
MATEYU 1:15
MATEYU 1:16
MATEYU 1:17
MATEYU 1:18
MATEYU 1:19
MATEYU 1:20
MATEYU 1:21
MATEYU 1:22
MATEYU 1:23
MATEYU 1:24
MATEYU 1:25
MATEYU 1 / MAT 1
MATEYU 2 / MAT 2
MATEYU 3 / MAT 3
MATEYU 4 / MAT 4
MATEYU 5 / MAT 5
MATEYU 6 / MAT 6
MATEYU 7 / MAT 7
MATEYU 8 / MAT 8
MATEYU 9 / MAT 9
MATEYU 10 / MAT 10
MATEYU 11 / MAT 11
MATEYU 12 / MAT 12
MATEYU 13 / MAT 13
MATEYU 14 / MAT 14
MATEYU 15 / MAT 15
MATEYU 16 / MAT 16
MATEYU 17 / MAT 17
MATEYU 18 / MAT 18
MATEYU 19 / MAT 19
MATEYU 20 / MAT 20
MATEYU 21 / MAT 21
MATEYU 22 / MAT 22
MATEYU 23 / MAT 23
MATEYU 24 / MAT 24
MATEYU 25 / MAT 25
MATEYU 26 / MAT 26
MATEYU 27 / MAT 27
MATEYU 28 / MAT 28