A A A A A
×

Chewa Bible 2014

MIYAMBO 25

1
Iyinso ndiyo miyambo ya Solomoni imene anthu a Hezekiya mfumu ya Yuda anailemba.
2
Kubisa kanthu ndi ulemerero wa Mulungu; koma ulemerero wa mafumu ndi kusanthula kanthu.
3
Pamlengalenga patalika, ndi padziko pakuya, koma mitima ya mafumu singasanthulike.
4
Chotsera siliva mphala yake, mmisiri wa ng'anjo atulutsamo mbale.
5
Chotsera woipa pamaso pa mfumu, mpando wake udzakhazikika m'chilungamo.
6
Usadzitame pamaso pa mfumu, ngakhale kuima m'malo mwa akulu.
7
Pakuti kunena kwa iwe, Takwera kuno, kupambana ndi kuti utsitsidwe pamaso pa kalonga, amene maso ako anamuona.
8
Usatuluke mwansontho kukalimbana, ungalephere pa kutha kwake, atakuchititsa mnzako manyazi.
9
Nena mlandu wako ndi mnzako, osawulula zinsinsi za mwini;
10
kuti wakumva angakutonze, mbiri yako yoipa ndi kusachoka.
11
Mau oyenera a pa nthawi yake akunga zipatso zagolide m'nsengwa zasiliva.
12
Monga mphete yagolide ndi chipini chagolide woyengeka, momwemo wanzeru wodzudzula pa khutu lomvera.
13
Monga chisanu cha chipale chofewa pa nthawi ya masika, momwemo mthenga wokhulupirika kwa amene anamtuma; atsitsimutsa moyo wa ambuyake.
14
Monga mitambo ndi mphepo popanda mvula, momwemo ndiye wodzikweza ndi zipatso zake monyenga.
15
Chipiriro chipembedza mkulu; lilime lofatsa lithyola fupa.
16
Wapeza uchi kodi? Idyapo wokwanira, kuti ungakukole, nusanze.
17
Phazi lako lilowe m'nyumba ya mnzako kamodzikamodzi; kuti angatope nawe ndi kukuda.
18
Wochitira mnzake umboni wonama ndiye chibonga, ndi lupanga, ndi muvi wakuthwa.
19
Kukhulupirira munthu wa chiwembu tsiku latsoka kunga dzino lothyoka ndi phazi loguluka.
20
Monga wovula malaya tsiku lamphepo, ngakhale kuthira vinyo wosasa m'soda, momwemo woimbira nyimbo munthu wachisoni.
21
Mdani wako akamva njala umdyetse, akamva ludzu ummwetse madzi.
22
Pakuti udzaunjika makala amoto pamtu pake; ndipo Yehova adzakupatsa mphotho.
23
Mphepo ya kumpoto ifikitsa mvula; chomwecho lilime losinjirira likwiyitsa nkhope.
24
Kukhala pangodya ya tsindwi kufunika kuposa kukhala m'nyumba ndi mkazi wolongolola.
25
Monga madzi ozizira kwa munthu wotopa, momwemo mau abwino akuchokera kudziko lakutali.
26
Monga kasupe wopondedwa, ndi chitsime choonongeka, momwemo wolungama ngati agonjera woipa.
27
Kudya uchi wambiri sikuli kwabwino; chomwecho kufunafuna ulemu wakowako sikuli ulemu.
28
Wosalamulira mtima wake akunga mudzi wopasuka wopanda linga.
MIYAMBO 25:1
MIYAMBO 25:2
MIYAMBO 25:3
MIYAMBO 25:4
MIYAMBO 25:5
MIYAMBO 25:6
MIYAMBO 25:7
MIYAMBO 25:8
MIYAMBO 25:9
MIYAMBO 25:10
MIYAMBO 25:11
MIYAMBO 25:12
MIYAMBO 25:13
MIYAMBO 25:14
MIYAMBO 25:15
MIYAMBO 25:16
MIYAMBO 25:17
MIYAMBO 25:18
MIYAMBO 25:19
MIYAMBO 25:20
MIYAMBO 25:21
MIYAMBO 25:22
MIYAMBO 25:23
MIYAMBO 25:24
MIYAMBO 25:25
MIYAMBO 25:26
MIYAMBO 25:27
MIYAMBO 25:28
MIYAMBO 1 / MIY 1
MIYAMBO 2 / MIY 2
MIYAMBO 3 / MIY 3
MIYAMBO 4 / MIY 4
MIYAMBO 5 / MIY 5
MIYAMBO 6 / MIY 6
MIYAMBO 7 / MIY 7
MIYAMBO 8 / MIY 8
MIYAMBO 9 / MIY 9
MIYAMBO 10 / MIY 10
MIYAMBO 11 / MIY 11
MIYAMBO 12 / MIY 12
MIYAMBO 13 / MIY 13
MIYAMBO 14 / MIY 14
MIYAMBO 15 / MIY 15
MIYAMBO 16 / MIY 16
MIYAMBO 17 / MIY 17
MIYAMBO 18 / MIY 18
MIYAMBO 19 / MIY 19
MIYAMBO 20 / MIY 20
MIYAMBO 21 / MIY 21
MIYAMBO 22 / MIY 22
MIYAMBO 23 / MIY 23
MIYAMBO 24 / MIY 24
MIYAMBO 25 / MIY 25
MIYAMBO 26 / MIY 26
MIYAMBO 27 / MIY 27
MIYAMBO 28 / MIY 28
MIYAMBO 29 / MIY 29
MIYAMBO 30 / MIY 30
MIYAMBO 31 / MIY 31