A A A A A
Facebook Instagram Twitter
Chewa Bible (BL) 1992

YOHANE 6١
Zitapita izi anacoka Yesu kunka ku tsidya lija la nyanja ya Galileya, ndiyo ya Tiberiya,
٢
Ndipo khamu lalikuru la anthu linamtsata iye, cifukwa anaona zizindikilo zimene anacita pa odwala.
٣
Koma Yesu anakwera kuphiri, nakhala pansi komweko pamodzi ndi akuphunzira ace.
٤
Ndipo Paskha, phwando la Ayuda, anayandikira.
٥
Pamenepo Yesu, pokweza maso ace, ndi kuona kuti khamu lalikuru lirinkudza kwa iye, ananena kwa Filipo, Tidzagula kuti mikate kuti adye awa?
٦
Koma ananena ici kuti amuyese; pakuti anadziwa yekha cimene adzacita.
٧
Filipo anayankha iye, Mikate ya marupiya atheka mazana awiri siikwanira iwo, kuti yense atenge pang'ono.
٨
Mmodzi wa akuphunzira ace, Andreya, mbale wace wa Simoni Petro, ananena ndi Iye,
٩
Pali mnyamata pano, amene ali nayo mikate isanu yabarele, ndi tinsomba tiwiri; koma nanga izi zifikira bwanji ambiri otere?
١٠
N ati Yesu, Akhalitseni anthu pansi, Ndipo panali udzu wambiri pamalopo, Pamenepo amunawo anakhala pansi, kuwerenga kwao monga zikwi zisanu.
١١
Pomwepo Yesu anatenga mikateyo; ndipo pamene adayamika, anagawira iwo akukhala pansi; momwemonso ndi tinsomba, monga momwe iwo anafuna.
١٢
Ndipo pamene adakhuta, Iyeananena kwa akuphunzira ace, Sonkhanitsani makombo kuti kasatayike kanthu.
١٣
Pomwepo anasonkhanitsa, nadzaza mitanga khumi ndi iwiri ndi makombo a mikate isanuyo yabarele, amene anatsalira anadyawo.
١٤
Cifukwa cace, anthu, poona cizindikilo cimene anacita, ananena, kuti, Ameneyo ndiye mneneri ndithu wakudzayom'dziko lapansi.
١٥
Pamenepo Yesu, pozindikira kuti alikufuna kudza kudzamgwira iye, kuti amlonge ufumu, anacokanso kunka kuphiri pa yekha.
١٦
Koma pofika madzulo, akuphunzira ace anatsikira kunyanja;
١٧
ndipo pamene adalowa m'ngalawa, analikuoloka nyanja kunka ku Kapernao. Ndipo kutada pamenepo, koma Yesu asanadze kwa iwo.
١٨
Ndipo nyanja inalikuuka cifukwa ca mphepo yaikulu yakuombako.
١٩
Ndipo parnene adapalasa monga mastadiya makumi awiri ndi asanu kapena makumi atatu, anaona Yesu alikuyenda panyanja, ndi kuyandikira ngalawa; ndipo anacita mantha.
٢٠
Koma iye ananena nao, ndine; musaope.
٢١
Pamenepo analola kumlandira m'ngalawa; ndipo pomwepo ngalawayo inafika kumtunda kumene analikunkako.
٢٢
M'mawa mwace khamu la anthu limene linaima tsidya lija la nyanja linaona kuti palibe ngalawa yina koma imodzi, ndi kuti Yesu sanalowa pamodzi ndi akuphunzira ace m'ngalawamo, koma akuphunzira ace adacoka pa okha;
٢٣
koma zinacokera ngalawa zina ku Tiberiya, pafupi pa malo pomwe adadyapo mkate m'mene Yesu adayamika;
٢٤
cifukwa cace pamene khamu la anthu linaona kuti palibe Yesu, ndi akuphunzira ace palibe, iwo okha analowa m'ngalawazo nadza ku Kapernao, alikufuna Yesu.
٢٥
Ndipo pamene anampeza iye tsidya lina la nyanja, anati kwa iye, Rabi, munadza kuno liti?
٢٦
Yesu anayankha iwo nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mundifuna Ine, si cifukwa munaona zizindikilo, koma cifukwa munadya mkate, nimunakhuta.
٢٧
Gwirani nchito si cifukwa ca cakudya cimene citayika koma ca cakudya cimene citsalira ku moyo wosatha, cimene Mwana wa munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera cizindikilo.
٢٨
Pamenepo anati kwa iye, Ticite ciani, kuti ticite nchito za Mulungu?
٢٩
Yesu anayankha nati kwa iwo, Nchito ya Mulungu ndi iyi, kuti mukhulupirire iye amene Iyeyo anamtuma.
٣٠
Cifukwa cace anati kwa iye, Ndipo mucita cizindikilo canji, kuti tione ndi kukhulupirira Inu? mucita ciani?
٣١
Atate athu anadya mana m'cipululu; monga kwalembedwa, Mkate wocokera m'mwamba anawapatsa iwo kudya,
٣٢
Cifukwa cace Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Si Mose amene anakupatsani inu mkate wa Kumwamba; koma Atate wanga akupatsani inu mkate woona wa Kumwamba.
٣٣
Pakuti mkate wa Mulungu ndiye wakutsika kucokera Kumwamba ndi kupatsa moyo kwa dziko lapansi.
٣٤
Pamenepo anati kwa iye, Ambuye, tipatseni ife mkate umene nthawi zonse.
٣٥
Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse.
٣٦
Koma ndinati kwa inu, kuti mungakhale mwandiona, simukhulupirira.
٣٧
Cinthu conse cimene anandipatsa Ine Atate cidzadza kwa Ine; ndipo wakudza kwa Ine sindidzamtaya iye kunja.
٣٨
Pakuti ndinatsika Kumwamba, si kuti ndicite cifuniro canga, koma cifuniro ca iye amene anandituma Ine.
٣٩
Koma cifuniro ca Iye amene anandituma Ine ndi ici, kuti za ici conse Iye anandipatsa Ine ndisatayeko kanthu, koma ndiciukitse tsiku lomariza.
٤٠
Pakuti cifuniro ca Atate wanga ndi ici, kuti yense wakuyang'ana Mwana, ndi kukhulupirira iye, akhale nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomariza.
٤١
Cifukwa cace Ayuda anang'ung'udza za iye, cifukwa anati, Ine ndine mkate wotsika Kumwamba.
٤٢
Ndipo iwo ananena, Si Yesu uyu, mwana wa Yosefe, atate wace ndi amai wace tiwadziwa? Anena bwanji tsopano, kuti, Ndinatsika Kumwamba?
٤٣
Yesu anayankha nati kwa iwo, Musang'ung'udze winandi mnzace.
٤٤
Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine amkoka iye; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomariza.
٤٥
Calembedwa mwa aneneri, Ndipo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi Mulungu. 1 Yense amene adamva kwa Atate, naphunzira, adza kwa Ine.
٤٦
2 Sikuti munthu wina waona Atate, koma 3 iye amene ali wocokera kwa Mulungu, ameneyo waona Atate.
٤٧
Indetu, indetu, ndinena ndi inu, 4 iye wokhuluplra ali nao moyo wosatha.
٤٨
5 Ine ndine mkate wamoyo,
٤٩
6 Makolo anu adadya m'cipululu, ndipo adamwalira.
٥٠
7 Mkate wotsika Kumwamba ndi uwu, kuti munthu akadyeko ndi kusamwalira.
٥١
8 Mkate wamoyo wotsika Kumwamba Ndine amene. Ngati munthu wina akadyako mkate umene, adzakhala ndi moyo kosatha. Inde, ndipo 9 mkate umene ndidzapatsa Ine, ndiwo thupi langa, ukhale moyo wa dziko lapansi.
٥٢
Pamenepo Ayuda anatetana wina ndi mnzace ndi kunena, Akhoza bwanji ameneyu kutipatsa ife kudya thupi lace?
٥٣
Cifukwa cace Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinenandi inu, 10 Ngati simukudya thupi la Mwana wa munthu ndi kumwa mwazi wace, mulibe moyo mwa inu nokha.
٥٤
11 Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomariza.
٥٥
Pakuti thupi langa ndi cakudya ndithu, ndi mwazi wanga ndi caku mwa ndithu.
٥٦
Iye wakudya thupi langa indi kumwa mwazi wanga 12 akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye.
٥٧
Monga Atate wamoyo anandituma Ine, ndipo Inenso ndiri ndi moyo cifukwa ca Atate; momwemo wondidya Ine, iyeyu adzakhala ndi moyo cifukwa ca Ine.
٥٨
13 Mkate wotsika Kumwamba ndi umenewu: si monga makolowo, anadya namwalira; iye wakudya mkate umene adzakhala ndi moyo nthawi zonse.
٥٩
Izi ananena m'sunagoge, pakuphunzitsa m'Kapernao.
٦٠
14 Pamenepo ambiri a akuphunzira ace, pakumva izi, anati, Mau awa ndi osautsa; akhoza kumva awa ndani?
٦١
Koma Yesu podziwa mwa yekha kuti akuphunzira ace alikung'ung'udza cifukwa ca ici, anati kwa iwo, ici mukhumudwa naco?
٦٢
15 Nanga bwanji ngati mukaona Mwana wa munthu alikukwera kumene anali kale lomwe?
٦٣
16 Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mau amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo.
٦٤
Koma 17 pali ena mwa inu amene sakhuluplra, Pakuti. Yesu anadziwa poyamba amene ali osakhulupira, ndi amene adzampereka.
٦٥
Ndipo ananena, 18 Cifukwa ca ici ndinati kwa inu, kuti palibe munthu angathe kudza kwa Ine, koma ngati kupatsidwa kwa Iye ndi Atate.
٦٦
19 Pa ici ambiri a akuphunzira ace anabwerera m'mbuyo, ndipo sanayenda-yendanso ndi iye.
٦٧
Cifukwa cace Yesu anati kwa khumi ndi awiriwo, Nanga inunso mufuna kucoka?
٦٨
Simoni Petro anamyankha iye, Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nao mau a moyo wosatha.
٦٩
Ndipo 20 ife tikhulupirira, ndipo tidziwa kuti Inu ndinu Woyera wa Mulungu.
٧٠
Yesu anayankha iwo, 21 Kodi sindinakusankhani khumi ndi awiri, ndipo mwa inu 22 mmodzi ali mdierekezi?
٧١
Koma adanena za Yudase, mwana wa Simoni Isikariote, pakuti iye ndiye amene akampereka iye, ali mmodzi wa khumi ndi awiri.YOHANE 6:1
YOHANE 6:2
YOHANE 6:3
YOHANE 6:4
YOHANE 6:5
YOHANE 6:6
YOHANE 6:7
YOHANE 6:8
YOHANE 6:9
YOHANE 6:10
YOHANE 6:11
YOHANE 6:12
YOHANE 6:13
YOHANE 6:14
YOHANE 6:15
YOHANE 6:16
YOHANE 6:17
YOHANE 6:18
YOHANE 6:19
YOHANE 6:20
YOHANE 6:21
YOHANE 6:22
YOHANE 6:23
YOHANE 6:24
YOHANE 6:25
YOHANE 6:26
YOHANE 6:27
YOHANE 6:28
YOHANE 6:29
YOHANE 6:30
YOHANE 6:31
YOHANE 6:32
YOHANE 6:33
YOHANE 6:34
YOHANE 6:35
YOHANE 6:36
YOHANE 6:37
YOHANE 6:38
YOHANE 6:39
YOHANE 6:40
YOHANE 6:41
YOHANE 6:42
YOHANE 6:43
YOHANE 6:44
YOHANE 6:45
YOHANE 6:46
YOHANE 6:47
YOHANE 6:48
YOHANE 6:49
YOHANE 6:50
YOHANE 6:51
YOHANE 6:52
YOHANE 6:53
YOHANE 6:54
YOHANE 6:55
YOHANE 6:56
YOHANE 6:57
YOHANE 6:58
YOHANE 6:59
YOHANE 6:60
YOHANE 6:61
YOHANE 6:62
YOHANE 6:63
YOHANE 6:64
YOHANE 6:65
YOHANE 6:66
YOHANE 6:67
YOHANE 6:68
YOHANE 6:69
YOHANE 6:70
YOHANE 6:71


YOHANE 1 / يوحنا 1
YOHANE 2 / يوحنا 2
YOHANE 3 / يوحنا 3
YOHANE 4 / يوحنا 4
YOHANE 5 / يوحنا 5
YOHANE 6 / يوحنا 6
YOHANE 7 / يوحنا 7
YOHANE 8 / يوحنا 8
YOHANE 9 / يوحنا 9
YOHANE 10 / يوحنا 10
YOHANE 11 / يوحنا 11
YOHANE 12 / يوحنا 12
YOHANE 13 / يوحنا 13
YOHANE 14 / يوحنا 14
YOHANE 15 / يوحنا 15
YOHANE 16 / يوحنا 16
YOHANE 17 / يوحنا 17
YOHANE 18 / يوحنا 18
YOHANE 19 / يوحنا 19
YOHANE 20 / يوحنا 20
YOHANE 21 / يوحنا 21