A A A A A
Facebook Instagram Twitter
Chewa Bible (BL) 1992

YOHANE 181
M'mene Yesu adanena izi, anaturuka ndi akuphunzira ace, kunka tsidya lija la mtsinje wa Kedroni, kumene kunali munda, umene analowamo iye ndi akuphunzira ace.
2
Koma Yudasenso amene akampereka iye, anadziwa malowa; cifukwa Yesu akamkako kawiri kawiri ndi akuphunzira ace.
3
Pamenepo Yudase, m'mene adatenga gulu la asilikari ndi anyamata, kwa ansembe akulu ndi Afarisi, anadza komweko ndi nyali ndi miuni ndi zida.
4
Pamenepo Yesu, podziwa zonse zirinkudza pa iye, anaturuka, nati kwa iwo, Mufuna yani?
5
Anayankha iye, Yesu Mnazarayo. Yesu ananena nao, Ndine. Koma Yudase yemwe, wompereka iye, anaima nao pamodzi.
6
Ndipo m'mene anati kwa iwo, Ndine, anabwerera m'mbuyo, nagwa pansi.
7
Pamenepo anawafunsanso, Mufuna yani? koma iwo anati, Yesu Mnazarayo.
8
Yesu anayankha, Ndati, Ndine; cifukwa cace ngati mufuna Ine, lekani awa amuke;
9
kuti akwaniridwe mau amene ati, Mwa iwo amene mwandipatsa Ine, sindinataya mmodzi.
10
Pamenepo Simoni Petro pokhala nalo lupanga, analisolola nakantha kapolo wa mkulu wa ansembe, namsenga khutu lace lamanja. Koma dzina lace la kapoloyo ndiye Malko.
11
Pamenepo Yesu anati kwa Petro, Longa Iupanga m'cimakecace; cikho cimene Atate wandipatsa Ine sindimwere ici kodi?
12
Ndipo khamulo ndi kapitao wamkuru, ndi anyamata a Ayuda anagwira Yesu nammanga iye,
13
nayamba kupita naye kwa Anasi; pakuti anali mpongozi wa Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe caka comweco.
14
Koma Kayafa anali uja wakulangiza Ayuda, kuti kuyenera munthu mmodzi afere anthu.
15
Koma Simoni Petro ndi wophunzira wina anatsata Yesu. Koma wophunzira ameneyo anali wodziwika kwa mkulu wa ansembe, nalowa pamodzi ndi Yesu, m'bwalo la mkulu wa ansembe;
16
koma Petro anaima kukhomo kunja, Cifukwa cace wophunzira winayo amene anadziwika kwa mkulu wa ansembe, anaturuka nalankhula ndi wapakhomo, nalowetsa Petro.
17
Pamenepo namwali wapakhomoyo ananena kwa Petro, Kodi suli iwenso wa akuphunzira a munthu uyu? Iyeyu ananena, Sindine.
18
Koma akapolo ndi anyamata analikuimirirako, atasonkha mota wamakara; pakuti kunali kuzizira; ndipo analikuotha moto; koma Petronso anali nao alikuimirira ndi kuotha moto.
19
Ndipo mkulu wa ansembe anafunsa Yesu za akuphunzira ace, ndi ciphunzitso cace.
20
Yesu anayankha iye, Ine ndalankhula zomveka kwa dziko lapansi; ndinaphunzitsa Ine nthawi zonse m'sunagoge ndi m'Kacisi, kumene amasonkhana Ayuda onse; ndipo mobisika sindinalankhula kanthu.
21
Undifunsiranji Ine? funsa iwo amene adamva cimene ndinalankhula nao; taona, amenewo adziwa cimene ndinanena Ine.
22
Koma m'mene iye adanena izi, mmodzi wa anyamata akuimirirako anapanda Yesu khofu, ndi kuti, Kodi uyankha mkulu wa ansembe comweco?
23
Yesu anayankha iye, Ngati ndalankhula coipa, cita umboni wa coipaco, koma ngati bwino, undipandiranji?
24
Koma Anasi adamtumiza iye womangidwa kwa Kayafa mkulu wa ansembe.
25
Koma Simoni Petro analikuimirira ndi kuotha moto. Pomwepo anati kwa iye, Suli iwenso wa akuphunzira ace kodi? Iyeyu anakana, nati, Sindine.
26
Mmodzi wa akapolo a mkulu wa ansembe ndiye mbale wace wa uja amene Petro anamdula khutu, ananena, Ine sindinakuona iwe kodi m'munda pamodzi ndi iye?
27
Pamenepo Petro anakananso; ndipo pomwepo analira tambala.
28
Pamenepo anamtenga Yesu kucokera kwa Kayafa kupita ku Pretorio; koma munali mamawa; ndipo iwo sanalowa ku Pretorio, kuti angadetsedwe, koma kuti akadye Paskha.
29
Cifukwa cace Pilato anaturukira kunja kwa iwo, nati, Cifukwa canji mwadza naco ca munthu uyu?
30
Anayankha nati kwa iye, Akadakhala wosacita zoipa uyu sitikadampereka iye kwa inu.
31
Ndipo Pilato anati kwa iwo, Mumtenge iye inu, ndi kumweruza iye monga mwa cilamulo canu. Ayuda anati kwa iye, Tiribe ulamuliro wakupha munthu ali yense;
32
kuti mau a Yesu akwaniridwe, amene ananena akuzindikiritsa imfa imene, akuti adzafa nayo.
33
Cifukwa cace Pilato analowanso m'Pretorio, naitana Yesu, nati kwa iye, Iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda kodi?
34
Yesu anayankha, Kodi munena ici mwa inu nokha, kapena ena anakuuzani za Ine?
35
Pilato anayankha, ndiri ine Myuda kodi? Mtundu wako ndi ansembe akulu anakupereka kwa ine; wacita ciani?
36
Yesu anayankha, Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wocokera konkuno.
37
Pamenepo Pilato anati kwa iye, Nanga kodi ndiwe Mfumu? Yesu anayankha, Munena kuti ndine Mfumu. Ndinabadwira ici Ine, ndipo ndinadzera ici kudza ku dziko lapansi, kuti ndikacite umboni ndi coonadi. Yense wakukhala mwa coonadi amva mau anga.
38
Pilato ananena kwa iye, Coonadi nciani? Ndipo pamene adanena ici, anaturukiranso kwa Ayudawo, nanena nao, vine sindipeza konse cifukwa mwa iye.
39
Koma muli nao makhalidwe, akuti ndimamasulira inu mmodzi pa Paskha; kodi mufuna tsono kuti ndimasulire inu Mfumu ya Ayuda?
40
Pomwepo anapfuulanso, nanena, Si uyu, koma Baraba. Koma Baraba anali wacifwamba.YOHANE 18:1
YOHANE 18:2
YOHANE 18:3
YOHANE 18:4
YOHANE 18:5
YOHANE 18:6
YOHANE 18:7
YOHANE 18:8
YOHANE 18:9
YOHANE 18:10
YOHANE 18:11
YOHANE 18:12
YOHANE 18:13
YOHANE 18:14
YOHANE 18:15
YOHANE 18:16
YOHANE 18:17
YOHANE 18:18
YOHANE 18:19
YOHANE 18:20
YOHANE 18:21
YOHANE 18:22
YOHANE 18:23
YOHANE 18:24
YOHANE 18:25
YOHANE 18:26
YOHANE 18:27
YOHANE 18:28
YOHANE 18:29
YOHANE 18:30
YOHANE 18:31
YOHANE 18:32
YOHANE 18:33
YOHANE 18:34
YOHANE 18:35
YOHANE 18:36
YOHANE 18:37
YOHANE 18:38
YOHANE 18:39
YOHANE 18:40


YOHANE 1 / YOH 1
YOHANE 2 / YOH 2
YOHANE 3 / YOH 3
YOHANE 4 / YOH 4
YOHANE 5 / YOH 5
YOHANE 6 / YOH 6
YOHANE 7 / YOH 7
YOHANE 8 / YOH 8
YOHANE 9 / YOH 9
YOHANE 10 / YOH 10
YOHANE 11 / YOH 11
YOHANE 12 / YOH 12
YOHANE 13 / YOH 13
YOHANE 14 / YOH 14
YOHANE 15 / YOH 15
YOHANE 16 / YOH 16
YOHANE 17 / YOH 17
YOHANE 18 / YOH 18
YOHANE 19 / YOH 19
YOHANE 20 / YOH 20
YOHANE 21 / YOH 21