1 |
Koma panali munthu wodwala, Lazaro wa ku Betaniya, wa m'mudzi wa Mariya ndi mbale wace Marita. |
2 |
Koma ndiye Mariya uja anadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira bwino, napukuta mapazi ace ndi tsitsi lace, amene mlongo wace Lazaro anadwala. |
3 |
Pamenepo alongo ace anatumiza kwa iye, nanena, Ambuye, onani, amene mumkonda adwala. |
4 |
Koma Yesu pamene anamva, anati, Kudwala kumene sikuli kwa imfa, koma cifukwa ca ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe nako. |
5 |
Koma Yesu anakonda Marita, ndi mbale wace, ndi Lazaro. |
6 |
Cifukwa cace pamene anamva kuti anadwala, anakhala pamenepo pa malo pomwepo masiku awiri. |
7 |
Ndipo pambuyo pace ananena kwa akuphunzira ace, Tiyeni tipitenso ku Yudeya. |
8 |
Akuphunzira ananena ndi iye, Ambuye, Ayuda analikufuna kukuponyani miyala tsopano apa; ndipo munkanso komweko kodi? |
9 |
Yesu anayankha, Kodi sikuli maora khumi ndi awiri usana? Ngati munthu ayenda usana sakhumudwa, cifukwa apenya kuunika kwa dziko lino lapansi, |
10 |
Koma ngati munthu ayenda usiku, akhumudwa, cifukwa mulibe kuunika mwa iye. |
11 |
Izi anati, ndipo zitatha izi ananena nao, Lazaro bwenzi lathu ali m'tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo tace. |
12 |
Cifukwa cace akuphunzira ace anati kwa iye, Ambuye, ngati ali m'tulo adzacira. |
13 |
Koma Yesu adanena za imfa yace; koma iwowa anayesa kuti ananena za mpumulo wa tulo. |
14 |
Pamenepo Yesu anati kwa iwo momveka, Lazaro wamwalira. |
15 |
Ndipo ndikondwera cifukwa ca inu kuti kunalibe Ine komweko, cakuti mukakhulupire; koma tiyeni, tipite kwa iye. |
16 |
Pamenepo Tomasi, wochedwa Didimo, anati kwa akuphunzira anzace, Tipite ifenso kuti tikafere naye pamodzi. |
17 |
Ndipo pamene Yesu anadza, anapeza kuti pamenepo atakhala m'manda masiku anai. |
18 |
Koma Betaniya anali pafupi pa Yerusalemu, nthawi yace yonga ya mastadiya khumi ndi asanu; |
19 |
koma ambiri a mwa Ayuda adadza kwa Marita ndi Mariya, kudzawatonthoza mtima pa mlongo wao. |
20 |
Pamenepo Marita, pakumva kuti Yesu alinkudza, anamuka kukakomana ndi iye; koma Mariya anakhalabe m'nyumba. |
21 |
Ndipo Marita anati kwa Yesu, Ambuye, mukadakhala kuno mlongo wanga sakadafa. |
22 |
Koma ngakhale tsopano ndidziwa kuti zinthu ziri zonse mukapempha Mulungu, adzakupatsani Mulungu. |
23 |
Yesu ananena naye, Mlongo wako adzauka. |
24 |
Marita ananena ndi iye, Ndidziwa kuti adzauka m'kuuka tsiku lomariza. |
25 |
Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo; wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo; |
26 |
ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse. Kodi ukhulupirira ici? |
27 |
Ananena ndi iye, Inde Ambuye; ndakhulupirira ine kuti Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu, wakudza m'dziko lapansi. |
28 |
Ndipo m'mene anati ici anacoka naitana Mariya mbale wace m'tseri, ndi kuti, Wafika Mphunzitsi, akuitana iwe. |
29 |
Koma iyeyo, pakumva, ananyamuka msanga, nadza kwa iye. |
30 |
(Koma Yesu sanafike kumudzi, koma anali pamalo pomwe Marita adakomana ndi Iye) |
31 |
Pamenepo Ayuda okhala naye m'nyumba, ndi kumtonthoza iye, pakuona Mariya ananyamuka msanga, naturuka, namtsata iye, ndi kuyesa kuti amuka kumanda kukalira komweko. |
32 |
Pomwepo Mariya, pofika pamene panali Yesu, m'mene anamuona iye, anagwa pa mapazi ace, nanena ndi iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira. |
33 |
Pamenepo Yesu, pakumuona iye alikulira, ndi Ayuda akumperekeza iye alikulira, anadzuma mumzimu, nabvutika mwini, |
34 |
nati, Mwamuika iye kuti? Ananena ndi iye, Ambuye, tiyeni, mukaone. |
35 |
Yesu analira. |
36 |
Cifukwa cace Ayuda ananena, Taonani, anamkondadi! |
37 |
Koma ena mwa iwo anati, Kodi uyu wotsegulira maso wosaona uja, sanakhoza kodi kucita kuti sakadafa ameneyunso? |
38 |
Pamenepo Yesu, ndi kudzumanso mwa iye yekha anadza kumanda. Koma panali phanga, ndipo mwala unaikidwa pamenepo. |
39 |
Yesu ananena, Cotsani mwala. Marita, mlongo wace wa womwalirayo, ananena ndi iye, Ambuye, adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anai. |
40 |
Yesu ananena naye, Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupira, udzaona ulemerero wa Mulungu? |
41 |
Pomwepo anacotsa mwala. Kama Yesu anakweza maso ace kupenya kumwamba nati, Atate, ndiyamika Inu kuti munamva Ine. |
42 |
Koma ndadziwa Ine kuti mumandimva Ine nthawi zonse; koma cifukwa ca khamu la anthu alikuimirira pozungulira ndinanena ici, kuti akhulupire kuti Inu munandituma Ine. |
43 |
Ndipom'mene adanena izi, ana pfuula ndi mau akuru, Lazaro, turuka. |
44 |
Ndipo womwalirayo anaturuka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsaru za kumanda; ndi nkhope yace inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nao, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke. |
45 |
Cifukwa cace ambiri a mwa Ayuda amene anadza kwa Mariya, m'mene anaona cimene anacita, anakhulupirira iye. |
46 |
Koma ena a mwa iwo anamuka kwa Afarisi, nawauza zimene Yesu adazicita. |
47 |
Pamenepo ansembe akulu ndi Afarisi anasonkhanitsa akulu, nanena, Titani ife? cifukwa munthu uyu acita zizindikilo zambiri. |
48 |
Ngati timleka iye kotero, onse adzakhulupirira iye; ndipo adzadza Aroma nadzacotsa malo athu ndi mtundu wathu. |
49 |
Koma wina mmodzi wa mwa iwo, Kayafa, wokhaia mkulu wa ansembe caka comweco anati kwa iwo, Simudziwa kanthu konse inu, |
50 |
kapena simuganiza kuti nkokoma kwa inu kuti munthu mmodzi afere anthu, ndi kuti mtundu wonse usaonongeke, |
51 |
Koma ici sananena kwa iye yekha; koma pokhala mkulu wa ansembe caka comweco ananenera kuti Yesu akadzafera mtunduwo; |
52 |
ndipo si cifukwa ca mtunduwo wokha ai, koma kuti akasonkhanitse pamodzi ana a Mulungu akubalalikawo. |
53 |
Cifukwa cace, kuyambira tsiku Iomwelo anapangana kuti amuphe iye. |
54 |
Cifukwa cace Yesu sanayandeyendanso poonekera mwa Ayuda, koma anacokapo kunka ku dziko loyandikira cipululu, kumudzi dzina lace Efraimu; nakhala komweko pamodzi ndi akuphunzira ace. |
55 |
Koma Paskha wa Ayuda anali pafupi; ndipo ambiri anakwera kunka ku Yerusalemu kucoka ku miraga, usanafike Paskha, kukadziyeretsa iwo okha. |
56 |
Pamenepo analikumfuna Yesu, nanena wina ndi mnzace poimirira iwo m'Kacisi, Muyesa bwanji inu, sadzadza kuphwando kodi? |
57 |
Koma ansembe akulu ndi Afarisi adalamulira, kuti, munthu wina akadziwa pokhala iye, aulule, kuti akamgwire iye.
|
Chewa Bible (BL) 1992 |
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society |
|
|
|
|
|
|
|
|
|
|
YOHANE 11:1 |
YOHANE 11:2 |
YOHANE 11:3 |
YOHANE 11:4 |
YOHANE 11:5 |
YOHANE 11:6 |
YOHANE 11:7 |
YOHANE 11:8 |
YOHANE 11:9 |
YOHANE 11:10 |
YOHANE 11:11 |
YOHANE 11:12 |
YOHANE 11:13 |
YOHANE 11:14 |
YOHANE 11:15 |
YOHANE 11:16 |
YOHANE 11:17 |
YOHANE 11:18 |
YOHANE 11:19 |
YOHANE 11:20 |
YOHANE 11:21 |
YOHANE 11:22 |
YOHANE 11:23 |
YOHANE 11:24 |
YOHANE 11:25 |
YOHANE 11:26 |
YOHANE 11:27 |
YOHANE 11:28 |
YOHANE 11:29 |
YOHANE 11:30 |
YOHANE 11:31 |
YOHANE 11:32 |
YOHANE 11:33 |
YOHANE 11:34 |
YOHANE 11:35 |
YOHANE 11:36 |
YOHANE 11:37 |
YOHANE 11:38 |
YOHANE 11:39 |
YOHANE 11:40 |
YOHANE 11:41 |
YOHANE 11:42 |
YOHANE 11:43 |
YOHANE 11:44 |
YOHANE 11:45 |
YOHANE 11:46 |
YOHANE 11:47 |
YOHANE 11:48 |
YOHANE 11:49 |
YOHANE 11:50 |
YOHANE 11:51 |
YOHANE 11:52 |
YOHANE 11:53 |
YOHANE 11:54 |
YOHANE 11:55 |
YOHANE 11:56 |
YOHANE 11:57 |
|
|
|
|
|
|
YOHANE 1 / YOH 1 |
YOHANE 2 / YOH 2 |
YOHANE 3 / YOH 3 |
YOHANE 4 / YOH 4 |
YOHANE 5 / YOH 5 |
YOHANE 6 / YOH 6 |
YOHANE 7 / YOH 7 |
YOHANE 8 / YOH 8 |
YOHANE 9 / YOH 9 |
YOHANE 10 / YOH 10 |
YOHANE 11 / YOH 11 |
YOHANE 12 / YOH 12 |
YOHANE 13 / YOH 13 |
YOHANE 14 / YOH 14 |
YOHANE 15 / YOH 15 |
YOHANE 16 / YOH 16 |
YOHANE 17 / YOH 17 |
YOHANE 18 / YOH 18 |
YOHANE 19 / YOH 19 |
YOHANE 20 / YOH 20 |
YOHANE 21 / YOH 21 |