English
A A A A A
×

Chewa Bible (BL) 1992

MATEYU 22
1
Ndipo Yesn anayankha, nalankhulanso kwa iwo m'mafanizo, nati,
2
Ufumu wa Kumwamba ufanafana ndi munthu, mfumu, amene anakonzera mwana wace phwando la ukwati,
3
natumiza akapolo ace kukaitana oitanidwa ku ukwati umene; ndipo iwo sanafuna kudza.
4
Pomwepo anatumizanso akapolo ena, nanena, Uzani oitanidwawo, Onani, ndakonza phwando langa; ng'ombe zanga, ndi zonona ndinazipha, ndi zinthu zonse zapsya: idzani kuukwati.
5
Koma iwo ananyalanyaza, nacoka, wina ku munda wace, wina ku malonda ace:
6
ndipo otsala anagwira akapolo ace, nawacitira cipongwe, nawapha.
7
Koma mfumu inakwiya; nituma asilikari ace napululutsa ambanda aja, nitentha mudzi wao.
8
Pomwepo inanena kwa akapolo ace, Za ukwati tsopano zapsya, koma oitanidwawo sanayenera.
9
Cifukwa cace pitani inu ku mphambano za njira, ndipo amene ali yense mukampeze, itanani kuukwatiku.
10
Ndipo akapolo ao anaturukira kunjira, nasonkhanitsa onse amene anawapeza, ngakhale oipa, ngakhale abwino; ndipo ukwatiwo unadzala ndi okhala pacakudya.
11
Koma mfumuyo m'mene inadza kuwaona akudyawo, anapenya momwemo munthu wosabvala cobvala ca ukwati;
12
nanena kwa iye, Mnzangawe, unalowa muno bwanji wosakhala naco cobvala ca ukwati? Ndipo iye analibe mau.
13
Pomwepo mfumu inati kwa atumiki, Mumange iye manja ndi miyendo, mumponye ku mdima wakunja; komweko kudzali kulira ndi kukukuta mano.
14
Pakuti oitanidwa ndiwo ambiri, koma osankhidwa ndiwo owerengeka.
15
Pomwepo Afarisi anamuka, nakhala upo wakumkola Iye m'kulankhula kwace.
16
Ndipo anatumiza kwa Iye ophunzira ao, pamodzi ndi Aherode, amene ananena, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo muphunzitsa njira ya Mulungu moona ndithu, ndipo simusamala munthu ali yense; pakuti simuyang'anira pa nkhope ya anthu.
17
Cifuka cace mutiuze ife, muganiza ciani? Kuloledwa kodi kupatsa msonkho kwa Kaisara, kapena iai?
18
Koma Yesu anadziwa kuipa kwao, nati, Mundiyeseranji Ine, onyenga inu?
19
Tandionetsani Ine ndalama yamsonkho. Ndipo iwo anadza nalo kwa Iye rupiya latheka.
20
Ndipo Iye anati kwa iwo, Nca yani cithunzithunzi ici, ndi kulemba kwace?
21
Nanena iwo, Ca Kaisara. Pomwepo Iye anati kwa iwo, Cifukwa cace patsani kwa Kaisara zace za Kaisara, ndi kwa Mulungu zace za Mulungu.
22
Ndipo pamene iwo anamva, anazizwa, namsiya Iye, nacokapo.
23
Tsiku lomwelo anadza kwa Iye Asaduki, amene amanena kuti palibe kuuka kwa akufa; namfunsa Iye,
24
nanena, Mphunzitsi, Mose anati, Ngati munthu akafa wopanda mwana, mphwace adzakwatira mkazi wace, nadzamuukitsira mbale wace mbeu.
25
Tsono panali ndi ife abale asanu ndi awiri; ndipo wakuyamba anakwatira, namwalira wopanda mbeu, nasiyira mphwace mkazi wace;
26
cimodzimodzi waciwiri, ndi wacitatu, kufikira wacisanu ndi ciwiri.
27
Ndipo pomarizira anamwaliranso mkaziyo.
28
Cifukwa cace m'kuuka kwa akufa, iye adzakhala mkazi wa yani wa asanu ndi awiriwo? pakuti onse anakhala naye.
29
Koma Yesu anayankha, nati kwa iwo, Mungolakwa a osadziwa malembo, kapena mphamvu za Mulungu.
30
Pakuti m'kuuka kwa akufa sakwatira, kapena kukwatiwa, koma akhala ngati angelo a Kumwamba.
31
Koma za kuuka kwa akufa, simunawerenga kodi comwe cinanenedwa kwa inu ndi Mulungu, kuti,
32
Ine ndiri Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo? Sali Mulungu wa akufa koma wa amoyo.
33
Ndipo pamene makamu a anthu anamva, anazizwa ndi ciphunzitso cace.
34
Koma Afarisi, pakumva kuti Iye anatontholetsa Asaduki, anasonkhana.
35
Ndipo mmodzi wa iwo, mphunzitsi wa cilamulo, anamfunsa ndi kumuyesa Iye, nati,
36
Mphunzitsi, lamulo lalikuru ndi liti la m'cilamulo?
37
Ndipo Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.
38
Ili ndilo lamulo lalikuru ndi loyamba.
39
Ndipo laciwiri lolingana nalo ndili, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.
40
Pa malamulo awa awiri mpokolowekapo cilamulo conse ndi aneneri.
41
Ndipo pamene Afarisi anasonkhana, Yesu anawafunsa,
42
nati, Muganiza bwanji za Kristu? ali mwana wa yani? Iwo ananena kwa Iye, Wa Davide.
43
Iye anati kwa iwo, Ndipo Davide mu Mzimu amchula Iye bwanji Ambuye, nanena,
44
Ambuye ananena kwa Ambuye wanga, Ukhale pa dzanja lamanja langa, Kufikira Ine ndidzaika adani ako pansi pa mapazi ako.
45
Cifukwa cace ngati Davide amchula Iye Ambuye, ali mwana wace bwanji? Ndipo panalibe mmodzi anatha kumyankha mau.
46
Ndipo sanalimbika mtima munthu ali yense kumfunsa kanthu kuyambira tsiku lomwelo.