A A A A A
×

Chewa Bible (BL) 1992

AHEBRI 9

1
Ndipo cingakhale cipangano coyambaci cinali nazo zoikika za kulambira, ndi malo opatulika a pa dziko lapansi.
2
Pakuti cihema cidakonzeka, coyamba cija, m'menemo munali coikapo nyali, ndi gome, ndi mkate woonekera; paja paitanidwa Malo Opatulika,
3
Koma m'kati mwa cophimba caciwiri, cihema conenedwa Malo Opatulikitsa;
4
okhala nayo mbale ya zofukiza yagolidi ndi likasa la cipangano, lokuta ponsepo ndi golidi, momwemo munali mbiya yagolidi yosungamo mana, ndi ndodo ya Aroni idapukayo, ndi magome a cipangano;
5
ndi pamwamba pace akerubi a ulemerero akucititsa mthunzi pacotetezerapo; za izi sitikhoza kunena tsopano padera padera.
6
Ndipo izi zitakonzeka kotero, ansembe amalowa m'cihema coyamba kosalekeza, ndi kutsiriza kulambirako;
7
koma kulowa m'caciwiri, mkuru wa ansembe yekha kamodzi pacaka, wosati wopanda mwazi, umene apereka cifukwa ca iye yekha, ndi zolakwa za anthu;
8
Mzimu Woyera wodziwitsa nako, kuti njira yolowa nayo ku malo opatulika siinaonetsedwe, pokhala cihema coyamba ciri ciriri;
9
ndico ciphiphiritso ca ku nthawi yomweyi, m'mene mitulo ndi nsembenso zinaperekedwa zosakhoza, ponena za cikumbu mtima, kuyesa wangwiro wolambirayo.
10
Popeza akhala zoikika za thupi zokha (ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe osiyana-siyana), oikidwa kufikira nthawi yakukonzanso.
11
Koma atafika Kristu, Mkuluwansembe wa zokoma zirinkudza, mwa cihema cacikuru ndi cangwiro coposa, cosamangika ndi manja, ndiko kunena kuti, cosati ca ciiengedweici,
12
kapena mwa mwazi wa mbuzi ndi ana a ng'ombe, koma mwa mwazi wa iye yekha, analowa kamodzi ku malo opatulika, atalandirapo ciombolo cosatha.
13
Pakuti ngati mwazi wa mbuzi ndi ng'ombe zamphongo, ndi makala a ng'ombe yamthandi owazawaza pa iwo odetsedwa, upatutsa kufikira ciyeretso ca thupi;
14
koposa kotani nanga mwazi wa Kristu amene anadzipereka yekha wopanda cirema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa cikumbu mtima canu kucisiyanitsa ndi nchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?
15
Ndipo mwa ici ali Nkhoswe ya cipangano catsopano, kotero kuti, popeza kudacitika imfa yakuombola zolakwa za pa cipangano coyamba, oitanidwawo akalandire lonjezano la zolowa zosatha.
16
Pakuti pamene pali copangiratu pafunika pafike imfa ya wolemberayo.
17
Pakuti copangiratu ciona mphamvu atafa mwini wace; popeza ciribe mphamvu konse pokhala wolemberayo ali ndi moyo;
18
momwemo coyambaconso sicinakonzeka copanda mwazi.
19
Pakuti pamene Mose adalankhulira anthu once lamulo liri lonse monga mwa cilamulo, anatenga mwazi wa ana a ng'ombe ndi mbuzi, pamodzi ndi madzi ndi ubweya wofiira ndi hisope, nawaza buku lomwe, ndi anthu onse,
20
nati, 1 Uwu ndi mwazi wa cipangano Mulungu adakulamulirani.
21
Ndiponso cihema ndi zotengera zonse za utumikiro anaziwaza momwemo ndi mwaziwo.
22
Ndipo monga mwa cilamulo zitsala zinthu pang'ono zosayeretsedwa ndi mwazi, ndipo 2 wopanda kukhetsa mwazi kulibe kumasuka.
23
Pomwepo padafunika kuti 3 zifaniziro za zinthu za m'Mwamba ziyeretsedwe ndi izi; koma zam'mwamba zeni zeni ziyeretsedwe ndi nsembe zoposa izi.
24
Pakuti 4 Kristu sanalowa m'malo opatulika omangika ndi manja, akutsanza oonawo; komatu m'Mwamba momwe, 5 kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu cifukwa ca ife;
25
kosati kuti adzipereke yekha kawiri kawiri; 6 monga mkulu wa ansembe alowa m'malo opatulika caka ndi caka ndi mwazi wosati wace;
26
cikadatero, kukadamuyenera kumva zowawa kawiri kawiri kuyambira kuzika kwa dziko lapansi; kama tsopano 7 kamodzi pa citsirizo ca nthawizo waonekera kucotsa ucimo mwa nsembe ya iye yekha.
27
Ndipo popeza 8 kwaikikatu kwa anthu kufa kamodzi, ndipo 9 atafa, ciweruziro;
28
kotero 10 Kristunso ataperekedwa nsembe kamodzi kukasenza macimo a ambiri, 11 adzaonekera pa nthawi yaciwiri, wopanda ucimo, kwa iwo amene amlindirira, kufikira cipulumutso.
AHEBRI 9:1
AHEBRI 9:2
AHEBRI 9:3
AHEBRI 9:4
AHEBRI 9:5
AHEBRI 9:6
AHEBRI 9:7
AHEBRI 9:8
AHEBRI 9:9
AHEBRI 9:10
AHEBRI 9:11
AHEBRI 9:12
AHEBRI 9:13
AHEBRI 9:14
AHEBRI 9:15
AHEBRI 9:16
AHEBRI 9:17
AHEBRI 9:18
AHEBRI 9:19
AHEBRI 9:20
AHEBRI 9:21
AHEBRI 9:22
AHEBRI 9:23
AHEBRI 9:24
AHEBRI 9:25
AHEBRI 9:26
AHEBRI 9:27
AHEBRI 9:28
AHEBRI 1 / AHE 1
AHEBRI 2 / AHE 2
AHEBRI 3 / AHE 3
AHEBRI 4 / AHE 4
AHEBRI 5 / AHE 5
AHEBRI 6 / AHE 6
AHEBRI 7 / AHE 7
AHEBRI 8 / AHE 8
AHEBRI 9 / AHE 9
AHEBRI 10 / AHE 10
AHEBRI 11 / AHE 11
AHEBRI 12 / AHE 12
AHEBRI 13 / AHE 13