A A A A A
MATEYU 1
1
Buku lofotokoza za mʼbado wa Yesu Khristu mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu:
2
Abrahamu anabereka Isake, Isake anabereka Yakobo, Yakobo anabereka Yuda ndi abale ake.
3
Yuda anabereka Perezi ndi Zara, amene amayi awo anali Tamara. Perezi anabereka Hezironi, Hezironi anabereka Aramu.
Chewa Bible 2016

1
Buku la kubadwa kwa Yesu Khristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu.
2
Abrahamu anabala Isaki; ndi Isaki anabala Yakobo; ndi Yakobo anabala Yuda ndi abale ake;
3
ndi Yuda anabala Perezi ndi Zera mwa Tamara; ndi Perezi anabala Hezironi; ndi Hezironi anabala Ramu;
Chewa Bible 2014

1
BUKU la kubadwa kwa Yesu Kristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu.
2
Abrahamu anabala Isake; ndi Isake anabala Yakobo; ndi Yakobo anabala Yuda ndi abale ace;
3
ndi Yuda anabala Farese ndi Zara mwa Tamare; ndi Farese anabala Ezronu; ndi Ezronu anabala Aramu;
Chewa Bible (BL) 1992