A A A A A
Baibulo mu chaka chimodzi
Epulo 13

YOSWA 15:1-63
1. Chigawo cha dzikolo chimene mabanja a fuko la Yuda analandira chinafika ku malire ndi Edomu mpaka ku chipululu cha Zini kummwera kwenikweni.
2. Malire awo a kummwera anayambira kummwera kwenikweni kwa Nyanja ya Mchere,
3. kudutsa cha kummwera ku Akirabimu, nʼkupitirira mpaka ku Zini. Kuchokera pamenepo nʼkumapita cha kummwera kwa Kadesi Barinea, kudutsa Hezironi mpaka ku Adari ndi kutembenuka mpaka ku Karika.
4. Anapitirira mpaka ku Azimoni motsata mtsinje umene uli malire a Igupto mpaka ku nyanja. Awa ndiwo malire awo a kummwera.
5. Malire a kummawa anali Nyanja Yakufa mpaka kumene Yorodani amathira mu Nyanja ya Mchere. Malire a kumpoto anayambira kumene Yorodani amathirira nyanjayo,
6. napitirira mpaka ku Beti-Hogila ndi kupitirira kumpoto mpaka ku Beti-Araba. Anapitirira mpaka anakafika ku Mwala wa Bohani.
7. Ndipo malirewo anachokeranso ku chigwa cha Akori mpaka ku Debri, kuchokera ku chigwa cha Akori ndi kutembenukira kumpoto ku Giligala, dera limene linayangʼanana ndi msewu wa Adumimu kummwera kwa chigwa. Anapitirira mpaka ku madzi a ku Eni Semesi ndi kutulukira ku Eni Rogeli.
8. Ndipo anapitirira mpaka ku chigwa cha Hinomu mbali ya kummwera kwa mzinda wa Ayebusi (mzinda wa Yerusalemu). Kuchokera kumeneko anakwera mpaka pamwamba pa phiri kumadzulo kwa chigwa cha Hinomu cha kumpoto kwenikweni kwa chigwa cha Refaimu.
9. Ndipo anachokeranso pamwamba pa phiri, kukafika mpaka ku akasupe a ku Nepitowa, nadzatulukira ku mizinda ya phiri la Efroni, ndi kutsikira ku Baalahi (ndiye Kiriati Yearimu).
10. Kuchokera kumeneko anazungulira cha kumadzulo ku Baalahi mpaka ku phiri la Seiri. Anapitirira cha kumpoto kutsata phiri la Yearimu (lomwe ndi Kesaloni). Anapitirirabe kutsika ku Beti Semesi ndi kuwolokera ku Timna.
11. Malirewo anapitirira kumatsitso a mapiri chakumpoto kwa Ekroni, ndi kukhotera ku Sikeroni. Malirewo anadutsa phiri la Baalahi ndi kufika ku Yabineeli. Malirewo anathera ku nyanja.
12. Malire a mbali ya kumadzulo anali Nyanja Yayikulu. Awa ndi malire ozungulira malo amene anapatsidwa kwa mabanja a fuko la Yuda.
13. Potsata lamulo la Yehova, Yoswa anapereka kwa Kalebe mwana wa Yefune gawo lina la dziko la Yuda dera la Kiriati Ariba, limene ndi Hebroni. (Ariba anali gogo wa Aanaki).
14. Kuchokera ku Hebroni, Kalebe anathamangitsamo mafuko a Aanaki awa: Sesai, Ahimani ndi Talimai, zidzukulu za Aanaki.
15. Kuchokera kumeneko, Kalebe anakathira nkhondo anthu amene ankakhala ku Debri (mzindawu poyamba unkatchedwa Kiriati Seferi).
16. Tsono Kalebe anati, “Munthu amene angathire nkhondo mzinda wa Kiriati Seferi ndi kuwulanda, ndidzamupatsa mwana wanga Akisa kuti akhale mkazi wake.”
17. Otanieli, mwana wa mʼbale wa Kalebe, Kenazi, ndiye anawulanda. Choncho Kalebe anamupatsa mwana wake Akisa kuti akhale mkazi wake.
18. Tsiku lina atafika Akisayo, Otanieli anamuwumiriza mkazi wakeyo kuti apemphe munda kwa Kalebe abambo ake. Pamene Akisa anatsika pa bulu wake, Kalebe anamufunsa kuti, “Kodi ukufuna ndikuchitire chiyani.”
19. Iye anayankha kuti “Mundikomere mtima. Popeza mwandipatsa ku Negevi, kumalo kumene kulibe madzi, mundipatsenso akasupe amadzi.” Choncho Kalebe anamupatsa akasupe a kumtunda ndi a kumunsi.
20. Dziko limene mabanja a fuko la Yuda analandira ngati cholowa chawo ndi ili:
21. Mizinda yakummwera kwenikweni kwa fuko la Yuda yoyandikana ndi malire a Edomu anali: Kabizeeli, Ederi, Yaguri
22. Kina, Dimona, Adada
23. Kedesi, Hazori, Itinani
24. Zifi, Telemu, Bealoti,
25. Hazori-Hadata, Keriyoti Hezironi (ndiye kuti Hazori)
26. Amamu, Sema, Molada
27. Hazari-Gada, Hesimoni, Beti-Peleti
28. Hazari-Suwali, Beeriseba, Biziotiya,
29. Baalahi, Iyimu, Ezemu
30. Elitoladi, Kesili, Horima
31. Zikilagi, Madimena, Sanisana,
32. Lebaoti, Silihimu, Aini ndi Rimoni. Mizinda yonse inalipo 29 pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
33. Mizinda ya ku chigwa cha kumadzulo ndi iyi: Esitaoli, Zora, Asina
34. Zanowa, Eni-Ganimu, Tapuwa, Enamu,
35. Yarimuti, Adulamu, Soko, Azeka,
36. Saaraimu, Aditaimu, ndi Gederi (kapena Gederotaimu). Mizinda yonse inalipo 14 pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
37. Mizinda ina inali iyi: Zenani, Hadasa, Migidali-Gadi,
38. Dileani, Mizipa, Yokiteeli,
39. Lakisi, Bozikati, Egiloni,
40. Kaboni, Lahimasi, Kitilisi,
41. Gederoti, Beti-Dagoni, Naama ndi Makeda. Mizinda yonse pamodzi inalipo 16 pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
42. Mizinda ina inali iyi: Libina, Eteri, Asani,
43. Ifita, Asina, Nezibu,
44. Keila, Akizibu ndi Maresa, mizinda isanu ndi inayi pamodzi ndi midzi yake.
45. Panalinso Ekroni pamodzi ndi midzi yake;
46. komanso yonse imene inali mʼmbali mwa Asidodi ndi midzi yake kuyambira ku Ekroni mpaka ku Nyanja Yayikulu.
47. Panalinso mizinda ya Asidodi ndi Gaza pamodzi ndi midzi yawo. Malire ake anafika ku mtsinje wa Igupto mpaka ku Nyanja Yayikulu.
48. Mizinda ya kumapiri inali: Samiri, Yatiri, Soko,
49. Dana, Kiriati-Sana, (ndiye kuti Debri)
50. Anabu, Esitemo, Animu,
51. Goseni, Holoni ndi Gilo. Mizinda yonse pamodzi inali khumi ndi umodzi pamodzi ndi midzi yake.
52. Analandiranso mizinda iyi: Arabu, Duma, Esani,
53. Yanumu, Beti-Tapuwa, Afeki
54. Humita, Kiriati-Ariba (ndiye kuti Hebroni) ndi Ziori, mizinda isanu ndi inayi pamodzi ndi midzi yake.
55. Panalinso Maoni, Karimeli, Zifi, Yuta
56. Yezireeli, Yokideamu, Zanowa,
57. Kaini, Gibeya ndi Timna, mizinda khumi ndi midzi yake.
58. Mizinda ina inali: Halihuli, Beti Zuri, Gedori,
59. Maarati, Beti-Anoti ndi Elitekoni, mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yake
60. Panalinso Kiriati Baala (ndiye kuti Kiriati Yearimu) ndi Raba; mizinda iwiri pamodzi ndi midzi yake.
61. Mizinda ya ku chipululu inali iyi: Beti-Araba, Midini, Sekaka,
62. Nibisani, Mzinda wa Mchere ndi Eni Gedi, mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yake.
63. Koma Yuda sanathe kuthamangitsa Ayebusi amene amakhala ku Yerusalemu, ndipo mpaka lero Ayebusi akukhala komweko pamodzi ndi Ayudawo.

YOSWA 16:1-10
1. Dziko limene linapatsidwa kwa fuko la Yosefe linayambira ku mtsinje wa Yorodani ku Yeriko, kummawa kwa akasupe a Yeriko, ndiponso kuyambira mtsinje wa Yorodaniwo nʼkumakwera, kudutsa mʼchipululu mpaka ku mapiri a ku Beteli.
2. Kuchokera ku Beteli malire ake anakafika ku Luzi, kudutsa dziko la Ataroti kumene kumakhala Aariki.
3. Malirewo anatsikira cha kumadzulo kwa dziko la Yafuleti mpaka ku chigawo cha kumunsi kwa Beti-Horoni. Kuchokera kumeneko anapitirira mpaka ku Gezeri nʼkuthera ku Nyanja.
4. Choncho Manase ndi Efereimu, ana a Yosefe analandira cholowa chawo.
5. Dziko la mabanja a fuko la Efereimu ndi ili: Malire a dzikolo anachokera kummawa kwa Ataroti Adari mpaka ku mtunda kwa Beti-Horoni.
6. Malirewo anapitirira mpaka ku nyanja. Mikimetati anali kumpoto kwake. Kuchokera kumeneko anakhotera cha kummawa kuloza ku Taanati Silo ndi kudutsa kumeneko cha kummawa mpaka ku Yanowa.
7. Ndipo kuchokera ku Yanowa anatsikira ku Ataroti ndi Naara, nakafika ku Yeriko ndi kukathera ku mtsinje wa Yorodani.
8. Kuchokera ku Tapuwa anapita kumadzulo mpaka ku mtsinje wa Kana ndi kukathera ku nyanja. Dziko ili linali cholowa cha mabanja afuko la Efereimu,
9. kuphatikizapo mizinda yonse ndi midzi yake yopatsidwa kwa Efereimu, koma yokhala mʼkati mwa dziko la Manase.
10. Iwo sanapirikitse Akanaani amene amakhala ku Gezeri ndipo mpaka lero Akanaani akukhala pakati pa Aefereimu koma amagwira ntchito ngati akapolo.

MASALIMO 45:1-5
1. Kwa mtsogoleri wamayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe a “Maluwa a Kakombo.” Salimo la ana a Kora. Nyimbo ya pa ukwati. Mtima wanga watakasika ndi nkhani yokoma pamene ndikulakatula mawu anga kwa mfumu; lilime langa ndi cholembera cha wolemba waluso.
2. Inu ndinu abwino kwambiri kuposa anthu onse ndipo milomo yanu inadzozedwa ndi chikondi cha Mulungu chosasinthika, popeza Mulungu wakudalitsani kwamuyaya.
3. Mangirirani lupanga lanu mʼchiwuno mwanu, inu munthu wamphamvu; mudziveke nokha ndi ulemerero ndi ukulu wanu.
4. Mu ukulu wanu mupite mutakwera mwachigonjetso mʼmalo mwa choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo; dzanja lanu lamanja lionetsere ntchito zanu zoopsa.
5. Mivi yanu yakuthwa ilase mitima ya adani a mfumu, mitundu ya anthu igwe pansi pa mapazi anu.

MIYAMBO 14:4-5
4. Pakasowa ngʼombe zolima gome limakhala lopanda chakudya, koma pakakhala ngʼombe zamphamvu zakudya zimachulukanso.
5. Mboni yokhulupirika sinama, koma mboni yonyenga imayankhula zabodza.

LUKA 11:29-54
29. Pamene gulu la anthu limachuluka, Yesu anati, “Uno ndi mʼbado oyipa. Umafuna kuona chizindikiro chodabwitsa. Koma sadzachiona kupatula chizindikiro chija cha Yona.
30. Monga Yona uja anali chizindikiro kwa anthu ku Ninive, momwemonso Mwana wa Munthu adzakhala chizindikiro kwa anthu a mʼbado uno.
31. Mfumu yayikazi yakummwera idzayimirira tsiku lachiweruzo pamodzi ndi anthu a mʼbado uno ndipo idzawatsutsa, chifukwa iyo inachokera kumapeto a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomoni. Ndipo tsopano pano pali wina woposa Solomoni.
32. Anthu a ku Ninive adzayimirira tsiku lachiweruzo pamodzi ndi mʼbado uno ndipo adzawutsutsa, pakuti anatembenuka mtima ndi ulaliki wa Yona. Ndipo tsopano pano pali wina woposa Yona.
33. “Palibe amene amayatsa nyale ndi kuyiika pa malo poti sionekera, kapena pansi pa mtsuko. Mʼmalo mwake amayika pa choyikapo chake, kuti iwo amene akulowamo aone kuwunika.
34. Diso lanu ndi nyale ya thupi lanu. Pamene maso anu ali bwino, thupi lanu lonse limadzaza ndi kuwunika. Koma ngati ali oyipa, thupi lanunso ndi lodzaza ndi mdima.
35. Onetsetsani tsono, kuti kuwunika kuli mwa inu si mdima.
36. Choncho, ngati thupi lanu lonse ndi lodzaza ndi kuwunika, ndiye kuti palibe dera lina lili mdima, lonselo lidzakhala kuwunika, monga momwe kuwunika kwa nyale kumakuwalirani.”
37. Yesu atamaliza kuyankhula, Mfarisi wina anamuyitana kuti akadye naye. Tsono Yesu analowa mʼnyumba ndi kukhala podyera.
38. Mfarisiyo anadabwa atazindikira kuti Yesu anayamba kudya wosatsata mwambo wawo wakasambidwe ka mʼmanja.
39. Kenaka Ambuye anamuwuza kuti, “Inu Afarisi mumatsuka kunja kwa chikho ndi mbale, koma mʼkati mwanu ndi modzaza ndi kudzikonda ndi zoyipa.
40. Anthu opusa inu! Kodi amene anapanga zamʼkati sanapangenso zakunja?
41. Koma popereka kwa osauka, perekani chimene chili mʼkati ndipo chilichonse chidzakhala choyera.
42. “Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa mumapereka kwa Mulungu chakhumi cha timbewu tonunkhira, ndi timbewu tokometsera chakudya ndi mbewu zina zonse za mʼmunda, koma mumakana chilungamo ndi chikondi cha Mulungu. Mumayenera kuchita zomalizirazi osalekanso kuchita zoyambazi.
43. “Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa mumakonda mipando yofunika kwambiri mʼmasunagoge ndi malonje mʼmalo a pa msika.
44. “Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa muli ngati manda osawaka, amene anthu amangoyendapo, osawadziwa.”
45. Mmodzi mwa akatswiri a Malamulo anamuyankha Iye nati, “Aphunzitsi, pamene mukunena zinthu izi, mukutinyoza ifenso?”
46. Yesu anayankha kuti, “Tsoka kwa inunso akatswiri a Malamulo chifukwa mumawalemetsa anthu ndi mtolo umene iwo sangathe kunyamula, ndipo inu eni ake simutenga chala chanu kuti muwathandize.
47. “Tsoka kwa inu, chifukwa mumawaka manda a aneneri, komatu ndi makolo anu amene anawapha.
48. Tsono potero mumachitira umboni za zimene makolo anu anachita. Anapha aneneri, ndipo inu mumawaka manda awo.
49. Chifukwa cha ichi, Mulungu mu nzeru zake anati, ‘Ine ndidzawatumizira aneneri ndi atumwi, ena mwa iwo adzawapha ndipo ena adzawazunza.’
50. Choncho mʼbado uwu udzasenza magazi a aneneri onse amene anakhetsedwa kuyambira pachiyambi cha dziko,
51. kuyambira magazi a Abele kufikira magazi a Zakariya amene anaphedwa pakati pa guwa lansembe ndi malo opatulika. Inde, Ine ndikuwuzani inu, mʼbado uno udzasenza zonsezi.
52. “Tsoka kwa inu akatswiri a Malamulo, chifukwa mwachotsa kiyi wachidziwitso inu eni akenu musanalowemo, ndipo mwatsekerezanso iwo amene amalowa.”
53. Pamene Yesu anachokamo, Afarisi ndi aphunzitsi a Malamulo anayamba kumamutsutsa koopsa ndi kumupanikiza ndi mafunso,
54. pofuna kumukola muchina chilichonse chimene Iye angayankhule.