A A A A A
Baibulo mu chaka chimodzi
Epulo 12

YOSWA 13:1-33
1. Yoswa atakalamba Yehova anamuwuza kuti, Iwe tsopano wakalamba kwambiri, koma dziko losalandidwa lilipobe lalikulu.
2. “Madera amene atsala ndi awa: chigawo chonse cha Afilisti ndi Agesuri
3. kuchokera ku mtsinje wa Sihori kummawa kwa Igupto mpaka kumpoto kwa dziko la Ekroni. Madera onse amawerengedwa kuti ndi a Akanaani ngakhale amalamulidwa ndi mafumu asanu a Afilisti a ku Gaza, Asidodi, Asikeloni, Gati, Ekroni ndi Agiti, komanso ku Avimu ku chigawo cha kumpoto.
4. Dziko lina la Akanaani ndi Ameara limene lili mʼmanja mwa Asidoni mpaka ku Afeki, dziko limene linachitana malire ndi dziko la Aamori.
5. Palinso dziko lonse la Gebala ndi Lebanoni cha kummawa kuyambira ku Baala-Gadi pa tsinde pa phiri la Herimoni mpaka ku Lebo Hamati.
6. “Palinso anthu okhala mʼchigawo cha ku mapiri kuchokera ku Lebanoni mpaka ku Misirefoti-Maimu, Ine ndidzawapirikitsa pamene Aisraeli azidzalowa. Tsono uwagawire Aisraeli dziko limeneli kuti likhale cholowa chawo monga momwe ndakulamulira.
7. Tsopano ugawire dziko limeneli mafuko asanu ndi anayi ndiponso theka la fuko la Manase, kuti likhale cholowa chawo.”
8. Anthu a fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi pamodzi ndi theka lina la fuko la Manase analandira kale cholowa chawo chimene Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa. Cholowa chawocho chinali kummawa kwa mtsinje wa Yorodani.
9. Dziko lawolo linayambira ku Aroeri mzinda umene uli pafupi ndi chigwa cha Arinoni, ndiponso mzinda umene uli pakati pa chigwacho. Dzikolo linkaphatikizanso dera lonse lokwera kuyambira ku Medeba mpaka ku Diboni.
10. Linkaphatikizanso mizinda yonse ya mfumu Sihoni ya Aamori, imene inkalamulira mu Hesiboni, mpaka ku malire a Aamoni.
11. Dzikoli linaphatikizanso Giliyadi, dziko la anthu a ku Gesuri ndi Maaka, phiri lonse la Herimoni ndi dziko lonse la Basani mpaka ku Saleka.
12. Linaphatikizanso dziko la mfumu Ogi ya ku Basani imene imalamulira kuchokera ku Asiteroti ndi Ederi. Iye yekha ndiye anali mfumu ya Arefaimu amene anapulumuka. Mose anali atawagonjetsa anthu amenewa ndi kuwathamangitsira kutali.
13. Koma Aisraeli sanathamangitse anthu a ku Gesuri ndi Maaka, kotero iwowa amakhalabe pakati pawo mpaka lero.
14. Koma Mose sanapereke dziko kwa fuko la Alevi popeza zopereka zopatulika zimene anthu ankapereka kwa Yehova, Mulungu wa Israeli, ndizo zinali cholowa chawo monga Yehova anawalonjezera.
15. Mose anapereka gawo lina la dziko kwa mabanja a fuko la Rubeni.
16. Dziko lawo linayambira ku Aroeri mzinda umene uli pafupi ndi chigwa cha Arinoni, mʼmudzi wa pakati pa chigwa, ndiponso dera lonse lokwera mpaka ku Medeba.
17. Dzikolo linaphatikizanso Hesiboni ndi mizinda yake yonse, komanso mizinda monga Diboni, Bamoti Baala, Beti-Baala-Meoni,
18. Yahaza, Kedemoti, Mefaati.
19. Kiriataimu, Sibima, Zereti-Sahari, pa phiri limene lili mʼchigwa,
20. Beti-Peori, ku matsitso a Pisiga, ndiponso Beti-Yesimoti.
21. Dzikolo linaphatikizanso mizinda yonse ya ku madera okwera ndiponso dziko lonse la mfumu Sihoni ya Aamori amene ankalamulira kuchokera ku Hesiboni. Mose anamugonjetsa iye pamodzi ndi mafumu a Amidiyani awa: Evi, Rekemu, Zuri, Huri ndi Reba, mafumu amene anagwirizana ndi Sihoni. Onsewa analamulira dzikolo ngati nduna za Sihoni.
22. Kuwonjezera pa amene anaphedwa ndi nkhondo, Aisraeli anapha ndi lupanga Balaamu mwana wa Beori, amene amachita za matsenga.
23. Malire a fuko la Rubeni anali mtsinje wa Yorodani. Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yake zinapatsidwa kwa mabanja a fuko la Rubeni kuti akhale cholowa chawo.
24. Dera limene Mose anapereka kwa mabanja a fuko la Gadi ndi ili:
25. Dziko la Yazeri, mizinda yonse ya mu Giliyadi ndiponso theka la dziko la Amori kukalekezera ku Aroeri, kufupi ndi Raba;
26. ndiponso kuyambira ku Hesiboni mpaka ku Ramati-Mizipa, ndi Betonimu; ndiponso kuyambira ku Mahanaimu mpaka ku dziko la Debri.
27. Mu chigwa cha Yorodani analandiramo Beti-Haramu, Beti-Nimira, Sukoti ndi Zafoni pamodzi ndi dziko lonse la mfumu Sihoni ya ku Hesiboni. Malire ake a ku madzulo anali mtsinje wa Yorodani kufikira ku Nyanja ya Kinereti, kumpoto.
28. Mizinda ndi midzi imeneyi inali cholowa cha mabanja a fuko la Gadi.
29. Mose anali atapereka kale gawo lina la dziko limeneli kwa theka la mabanja a fuko la Manase kuti likhale cholowa chawo.
30. Derali linayambira ku Mahanaimu kuphatikizapo dziko lonse la mfumu Ogi, Mfumu ya ku Basani, pamodzi ndi mizinda 60 ya ku Yairi, ku Basaniko.
31. Derali linaphatikizanso theka la Giliyadi pamodzi ndi Asiteroti ndi Ederi, mizinda yayikulu ya mfumu Ogi wa Basani. Mizinda imeneyi inapatsidwa kwa mabanja a Makiri, mwana wa Manase kuti ikhale cholowa cha theka la ana a Makiri, malinga ndi mabanja awo.
32. Umu ndi mmene Mose anagawira malo a mʼchigwa cha Yorodani, kummawa kwa Yeriko, ku tsidya kwa Yorodani.
33. Komatu Mose sanapereke malo kwa fuko la Levi. Mose anawawuza kuti zopereka zimene anthu ankapereka kwa Yehova ndizo cholowa chawo.

YOSWA 14:1-15
1. Umu ndi mmene Aisraeli analandirira cholowa chawo mʼdziko la Kanaani. Eliezara wansembe, Yoswa mwana wa Nuni pamodzi ndi akuluakulu a mafuko a Israeli ndiwo anagawa dzikolo kugawira Aisraeli.
2. Madera anagawidwa mwa maere kwa mafuko asanu ndi anayi ndi theka, monga momwe Yehova analamulira kudzera mwa Mose.
3. Mose anapereka kwa mafuko awiri ndi theka dziko la kummawa kwa Yorodani, koma fuko la Levi lokha silinagawiridwe malo.
4. Tsono fuko la Yosefe analigawa pawiri, Manase ndi Efereimu. Mose sanawagawire malo mabanja a fuko la Levi, koma iwo anangolandira mizinda imene ankakhalamo pamodzi ndi malo amene ankawetako nkhosa ndi ngʼombe zawo.
5. Choncho Aisraeli anagawana dzikolo, monga momwe Yehova analamulira Mose.
6. Tsono anthu a fuko la Yuda anabwera kwa Yoswa ku Giligala, ndipo Kalebe mwana wa Yefune Mkeni anati kwa iye, “Inu mukudziwa zimene Yehova ananena kwa Mose munthu wa Mulungu za inu ndi ine ku Kadesi Barinea.
7. Nthawi imene Mose mtumiki wa Yehova anandituma kuchokera ku Kadesi Barinea kudzayendera dzikoli ndinali ndi zaka makumi anayi. Ndipo nditabwerako ndinamuwuza zoona zokhazokha monga momwe ndinaonera.
8. Koma abale anga amene ndinapita nawo anachititsa anthu mantha. Komabe ine ndinamvera Yehova Mulungu wanga ndi mtima wonse.
9. Kotero tsiku limenelo Mose anandilonjeza kuti, ‘Dziko limene unayendamo lidzakhala lako ndiponso la ana ako kwamuyaya chifukwa unamvera Yehova Mulungu wanga ndi mtima wako wonse.’
10. “Tsono papita zaka 45 chiyankhulire Yehova zimenezi kwa Mose. Nthawi imeneyo nʼkuti Aisraeli akuyendayenda mʼchipululu. Yehova wandisunga ndipo tsopano ndili ndi zaka 85.
11. Komabe ndikanali ndi mphamvu lero, monga ndinalili tsiku lija Mose anandituma. Ndili ndi mphamvu moti ndikhoza kupita ku nkhondo kapena kuchita kanthu kena kalikonse.
12. Tsopano ndipatseni dziko la ku mapiri limene Yehova anandilonjeza tsiku lija. Inu munamva nthawi ija kuti Aanaki anali kumeneko ndipo kuti mizinda yawo inali ikuluikulu ndi yotetezedwa. Komabe Yehova atakhala nane ndidzawathamangitsa monga Iye ananenera.”
13. Ndipo Yoswa anadalitsa Kalebe mwana wa Yefune ndi kumupatsa Hebroni kukhala dziko lake.
14. Choncho dera la Hebroni lakhala lili la Kalebe mwana wa Yefune Mkeni mpaka lero chifukwa anamvera Yehova Mulungu wa Israeli ndi mtima wonse.
15. (Hebroni ankatchedwa Kiriati Ariba chifukwa cha Ariba amene anali munthu wamphamvu kwambiri pakati pa Aanaki). Ndipo kenaka mʼdziko monse munakhala mtendere.

MASALIMO 44:20-26
20. Tikanayiwala dzina la Mulungu wathu kapena kutambasulira manja athu kwa mulungu wachilendo,
21. kodi Mulungu wathu sakanazidziwa zimenezi, pakuti Iye amadziwa zinsinsi zamumtima?
22. Komabe chifukwa cha Inu timakumana ndi imfa tsiku lonse, tili ngati nkhosa zoyenera kuti ziphedwe.
23. Dzukani Ambuye! Nʼchifukwa chiyani mukugona! Dziwutseni nokha! Musatikane kwamuyaya.
24. Nʼchifukwa chiyani mukubisa nkhope yanu, ndi kuyiwala mavuto athu ndi kuponderezedwa kwathu?
25. Tatsitsidwa pansi mpaka pa fumbi; matupi athu amatirira pa dothi.
26. Imirirani ndi kutithandiza, tiwomboleni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.

MIYAMBO 14:3-3
3. Kuyankhula kwa chitsiru kumamuyitanira ndodo pa msana, koma milomo ya munthu wanzeru imamuteteza.

LUKA 11:1-28
1. Tsiku lina Yesu amapemphera pamalo ena. Atamaliza, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa Iye, “Ambuye tiphunzitseni kupemphera, monga momwe Yohane anaphunzitsira ophunzira ake.”
2. Yesu anawawuza kuti, “Pamene mukupemphera muzinena kuti: “ ‘Atate, dzina lanu lilemekezedwe, ufumu wanu ubwere.
3. Mutipatse chakudya chathu chalero,
4. mutikhululukire machimo athu, monga ifenso timakhululukira aliyense amene watilakwira. Ndipo musalole kuti tigwe mʼmayesero.’ ”
5. Kenaka anawawuza kuti, “Tiyerekeze: Mmodzi mwa inu atakhala ndi bwenzi lake, ndipo iye nʼkupita ku nyumba yake pakati pa usiku, nakanena kuti, ‘Mnzanga, bwereke malofu atatu abuledi,
6. chifukwa ndalandira bwenzi langa amene ali pa ulendo ndipo ine ndilibe choti ndimupatse.’
7. “Ndipo yerekezani kuti amene ali mʼnyumbamo ndi kuyankha kuti, ‘Usandivutitse ine, ndatseka kale chitseko, ndipo ine ndi ana anga tagona. Ine sindingadzukenso kuti ndidzakupatse.’
8. Ine ndikukuwuzani kuti adzadzuka ndi kumupatsa bulediyo, osati chifukwa ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha liwuma la munthu wopemphayo, ndipo kudzamupatsa zonse zimene akuzifuna.
9. “Choncho Ine ndikunena kwa inu kuti: Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza. Gogodani ndipo adzakutsekulirani.
10. Pakuti aliyense amene amapempha amalandira. Munthu amene amafunafuna amapeza. Iye amene amagogoda amamutsekulira.
11. “Ndani mwa inu abambo, kodi mwana wanu atapempha nsomba, mʼmalo mwake mungamupatse njoka?
12. Kapena atapempha dzira, kodi mungamupatse chinkhanira?
13. Tsono ngati inu, anthu oyipa, mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, koposa kotani Atate anu akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene awapempha!”
14. Yesu amatulutsa chiwanda chimene chinali chosayankhula. Chiwandacho chitatuluka, munthu wosayankhulayo anayankhula, ndipo gulu la anthu linadabwa.
15. Koma ena mwa iwo anati, “Iye akutulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu mfumu ya ziwanda.”
16. Ena anamuyesa pomufunsa chizindikiro chochokera kumwamba.
17. Yesu anadziwa maganizo awo ndipo anawawuza kuti, “Ufumu uliwonse wogawikana udzawonongeka, ndipo nyumba yogawikana idzapasuka.
18. Ngati Satana adziwukira yekha, ufumu wake ungalimbe bwanji? Ine ndikunena izi chifukwa inu mukuti Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu.
19. Tsopano ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu, nanga ophunzira anu amazitulutsa ndi mphamvu ya ndani? Choncho, iwowo ndiye adzakhala oweruza anu.
20. Koma ngati ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Mulungu, ndiye kuti ufumu wa Mulungu wafika pakati panu.
21. “Munthu wamphamvu, amene ali ndi zida, akamalondera nyumba yake, katundu wake amatetezedwa.
22. Koma pakabwera wina wamphamvu zoposa namugonjetsa, amalanda zida zimene munthuyo amazidalirazo ndi kugawa katundu wake.
23. “Munthu amene sali mbali yanga ndi wotsutsana nane. Ndipo wosandithandiza kusonkhanitsa, ameneyo ndi womwaza.
24. “Mzimu woyipa ukatuluka mwa munthu, umakayendayenda ku malo owuma, kufunafuna malo opumulirako ndipo suwapeza. Kenaka umati, ‘Ndibwerera ku nyumba kwanga kumene ndachokera.’
25. Ukafika umapeza mʼnyumba mosesedwa bwino ndi mokonza.
26. Pamenepo umakatenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoyipa kwambiri kuposa iwowo ndipo imakalowa ndi kukhala mʼmenemo. Ndipo makhalidwe otsiriza a munthuyo amakhala oyipa kuposa oyamba aja.”
27. Pamene Yesu ankanena zonsezi, mayi wina mʼgulu la anthuwo anafuwula nati, “Ndi wodala amayi amene anakubalani ndi kukulerani!”
28. Koma Yesu anayankha kuti, “ Odala ndi amene amamva mawu a Mulungu ndi kuwasunga.”