A A A A A
Baibulo mu chaka chimodzi
Marichi 4

NUMERI 5:1-31
1. Yehova anawuza Mose kuti,
2. “Lamula Aisraeli kuti achotse mu msasa aliyense amene ali ndi matenda opatsirana a pa khungu kapena matenda otuluka madzi mʼthupi a mtundu uliwonse, kapena aliyense wodetsedwa chifukwa cha munthu wakufa.
3. Muchotse amuna komanso amayi ndipo muwatulutsire kunja kwa msasa kuti asadetse msasa wawo kumene Ine ndimakhala pakati pawo.”
4. Aisraeli anachitadi zimenezi. Anawatulutsira kunja kwa msasa monga momwe Yehova analamulira Mose.
5. Yehova anati kwa Mose,
6. “Uza Aisraeli kuti, ‘Pamene mwamuna kapena mayi walakwira mnzake mwa njira iliyonse, ndiye kuti ndi wosakhulupirika pamaso pa Yehova. Munthuyo ndi wochimwa ndithu ndipo
7. ayenera kuwulula tchimo limene anachitalo. Ayenera kubweza zonse zimene anawononga, ndipo awonjezerepo chimodzi mwa magawo asanu ndi kuzipereka kwa munthu amene anamulakwirayo.
8. Ngati wolakwiridwayo alibe mʼbale komwe kungapite zinthu zobwezedwazo, zinthuzo zikhale za Yehova ndipo azipereke kwa wansembe, pamodzi ndi nkhosa yayimuna ya nsembe yopepesera tchimo lake.
9. Zopereka zonse zopatulika zomwe Aisraeli abwera nazo kwa wansembe zikhale za wansembeyo.
10. Mphatso zilizonse zopatulika ndi za munthuyo, koma zomwe wapereka kwa wansembe ndi za wansembeyo.’ ”
11. Kenaka Yehova anawuza Mose kuti,
12. “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ngati mkazi wa munthu wina ayenda njira yosayenera nakhala wosakhulupirika kwa mwamuna wake,
13. nakagonana ndi mwamuna wina koma mwamuna wake wosadziwa, ndipo palibe wina aliyense wadziwa za kudzidetsa kwake (pakuti palibe mboni yomuneneza chifukwa sanagwidwe akuchita),
14. mwamuna wake ndi kuyamba kuchita nsanje ndi kukayikira mkazi wakeyo kuti ndi wodetsedwa, komanso ngati amuchitira nsanje ndi kumukayikira ngakhale asanadzidetse,
15. apite naye mkaziyo kwa wansembe. Ndipo popita atengenso gawo lakhumi la chopereka chaufa wa barele wokwana kilogalamu imodzi mʼmalo mwa mkaziyo. Asathire mafuta pa nsembeyo kapena lubani, chifukwa ndi nsembe ya chopereka ya chakudya yopereka chifukwa cha nsanje, nsembe yozindikiritsa tchimo.’ ”
16. “ ‘Wansembe abwere naye mkaziyo ndi kumuyimitsa pamaso pa Yehova.
17. Ndipo wansembeyo atenge madzi oyera mʼmbiya ya dothi ndi kuyika mʼmadzimo fumbi lapansi la mʼTenti ya Msonkhano.
18. Wansembe atayimika mkaziyo pamaso pa Yehova, amumasule tsitsi lake, ndipo ayike mʼmanja mwake nsembe yozindikiritsa tchimo, nsembe yachakudya ya nsanje, wansembeyo atanyamula madzi owawa omwe amabweretsa temberero.’
19. Kenaka wansembeyo alumbiritse mkaziyo ndi kuti, ‘Ngati mwamuna wina aliyense sanagonane ndi iwe ndipo sunayende njira yoyipa ndi kukhala wodetsedwa pomwe uli pa ukwati ndi mwamuna wako, madzi owawa awa omwe amabweretsa temberero asakupweteke.
20. Koma ngati wayenda njira yoyipa uli pa ukwati ndi mwamuna wako ndi kudzidetsa pogonana ndi mwamuna amene si mwamuna wako,’
21. pamenepo wansembe alumbiritse mkaziyo ndi mawu a matemberero ndi kumuwuza kuti, ‘Yehova achititse anthu ako kukutemberera ndi kukunyoza pamene awononga ntchafu yako ndi kutupitsa mimba yako.
22. Madzi awa obweretsa temberero alowe mʼthupi mwako ndi kutupitsa mimba yako ndi kuwononga ntchafu yako.’ ” “Pamenepo mkaziyo anene kuti, ‘Ameni, ameni.’ ”
23. “ ‘Wansembe alembe matemberero amenewa mʼbuku ndi kuwanyika mʼmadzi owawa aja.
24. Amwetse mkaziyo madzi owawawo omwe amabweretsa temberero, ndipo madzi amenewo adzalowa mʼmimba mwake ndi kuyambitsa ululu woopsa.
25. Wansembe achotse mʼmanja mwa mkaziyo nsembe yachakudya ya nsanje ija, nayiweyula pamaso pa Yehova ndi kuyipereka pa guwa lansembe.
26. Tsono wansembeyo atapeko ufa dzanja limodzi kuti ukhale wachikumbutso ndi kuwutentha pa guwa lansembe. Atatha izi, amwetse mkaziyo madzi aja.
27. Ndipo ngati mkaziyo anadzidetsadi ndi kukhala wosakhulupirika kwa mwamuna wake, pamene amwa madzi obweretsa matemberero aja, nalowa mʼmimba mwake, adzamva ululu woopsa. Mimba yake idzatupa ndi ntchafu yake idzawonongeka ndipo adzakhala wotembereredwa pakati pa anthu ake.
28. Koma ngati mkaziyo sanadzidetse ndi kuti alibe tchimo, adzakhala wopanda mlandu ndipo adzabereka ana.
29. “ ‘Limeneli ndiye lamulo la nsanje pamene mkazi wayenda njira yoyipa ndi kudzidetsa ali pa ukwati ndi mwamuna wake,
30. kapena pamene maganizo a nsanje abwera kwa mwamuna wake chifukwa chokayikira mkazi wakeyo. Wansembe azitenga mkazi wotere ndi kumuyimiritsa pamaso pa Yehova ndipo agwiritse ntchito lamulo lonseli kwa mkaziyo.
31. Mwamunayo adzakhala wopanda tchimo lililonse, koma mkaziyo adzasenza zotsatira za tchimo lake.’ ”

NUMERI 6:1-27
1. Yehova anawuza Mose kuti,
2. “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ngati mwamuna kapena mkazi afuna kuchita lonjezo lapadera, lonjezo lodzipatula yekha kwa Yehova ngati Mnaziri,
3. sayenera kumwa vinyo kapena zakumwa zosasa ndipo asamamwe chakumwa chilichonse cha mphesa. Asamamwe madzi a mphesa kapena kudya mphesa zaziwisi kapena zowuma.
4. Pa nthawi yonse imene ali Mnaziri, asamadye chilichonse chopangidwa kuchokera ku mphesa ngakhale mbewu zake kapena makungu ake.’
5. “ ‘Pa nthawi yonse ya lonjezo lodzipatula yekhalo, asamete kumutu kwake ndi lumo. Akhale wopatulika mpaka nthawi yake yonse ya kudzipatula yekha kwa Yehova itatha. Alileke tsitsi la pamutu pake kuti likule.’
6. Pa nthawi yonse imene munthuyo wadzipatula yekha kwa Yehova asayandikire mtembo.
7. Ngakhale abambo ake kapena amayi ake kapena mchimwene wake kaya mchemwali wake atamwalira, asadzidetse pokhudza mitembo yawo chifukwa kulumbira kwake kwa kudzipatula yekha kwa Yehova kuli pamutu pake.
8. Munthuyo ndi wopatulika masiku onse odzipereka kwake kwa Yehova.
9. “Ngati munthu wina afa mwadzidzidzi pafupi naye ndi kudetsa tsitsi lake loperekedwalo, amete mutu wake pa tsiku lodziyeretsa, tsiku lachisanu ndi chiwiri.
10. Tsono pa tsiku lachisanu ndi chitatu abweretse nkhunda ziwiri kapena mawunda awiri anjiwa kwa wansembe pa khomo lolowera ku tenti ya msonkhano.
11. Wansembe apereke imodzi kuti ikhale nsembe yauchimo ndi ina nsembe yopsereza yotetezera tchimo chifukwa anachimwa popezeka pafupi ndi mtembo. Ndipo tsiku lomwelo apatulenso tsitsi la pamutu pake.
12. Adzipereke kwa Yehova pa nthawi yodzipatula ndipo abweretse nkhosa yayimuna ya chaka chimodzi ngati nsembe yopepesera. Masiku akale sawerengedwanso chifukwa anadzidetsa pa nthawi yodzipatulira kwake.
13. “Tsono ili ndi lamulo la Mnaziri pamene nthawi yodzipatula kwake yatha: Abwere naye pa khomo la tenti ya msonkhano.
14. Pamenepo apereke chopereka chake kwa Yehova: Nkhosa yayimuna ya chaka chimodzi yopanda chilema kuti ikhale nsembe yopsereza, mwana wankhosa wamkazi mmodzi wopanda chilema kuti ikhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa imodzi yayikulu yayimuna kuti ikhale nsembe yachiyanjano,
15. ndipo abwere pamodzi ndi nsembe yachakudya ndi nsembe yachakumwa ndi dengu la buledi wopanda yisiti, makeke opangidwa ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda ta buledi topakidwa mafuta.
16. “Wansembe apereke zimenezi pamaso pa Yehova ndi kuchita nsembe ya uchimo ndi nsembe yopsereza.
17. Apereke dengu la buledi wopanda yisiti ndiponso nsembe yachiyanjano kwa Yehova ya nkhosa yayimuna, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi chopereka cha chakumwa.
18. “Mnaziriyo amete tsitsi limene analipereka lija pa khomo la tenti ya msonkhano. Atenge tsitsilo ndi kuliyika pa moto umene uli pansi pa nsembe yachiyanjano.
19. “Mnaziriyo atatha kumeta tsitsi analiperekalo, wansembe ayike mʼmanja mwake mwendo wa mmwamba wankhosa yayimuna umene waphikidwa ndipo atengenso keke ndi kamtanda ka buledi, zonse zopanda yisiti zomwe zili mʼdengu lija.
20. Wansembe aziweyule pamaso pa Yehova ngati nsembe yoweyula. Zimenezi ndi zopatulika ndipo ndi za wansembe pamodzi ndi chidale chimene anachiweyula ndi ntchafu yomwe anayipereka ija. Zitatha izi, Mnaziri akhoza kumwa vinyo.
21. “Ili ndi lamulo la Mnaziri yemwe walonjeza kudzipereka kwa Yehova podzipatula yekha kuphatikiza pa zomwe angathe kukwaniritsa. Ayenera kukwaniritsa lonjezo lomwe wachitalo potsata lamulo la Mnaziri.”
22. Yehova anawuza Mose kuti,
23. “Uza Aaroni ndi ana ake aamuna kuti, ‘Umu ndi mmene muzidalitsira Aisraeli. Muzinena kuti,
24. “ ‘Yehova akudalitse ndi kukusunga;
25. Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitira chisomo;
26. Yehova akweze nkhope yake pa iwe, nakupatse mtendere.’ ”
27. Choncho akadzatchula dzina langa podalitsa Aisraeli, Ine ndidzawadalitsadi.

MASALIMO 30:8-12
8. Kwa Inu Yehova ndinayitana; kwa Ambuye ndinapempha chifundo;
9. “Kodi pali phindu lanji powonongeka kwanga ngati nditsikira ku dzenje? Kodi fumbi lidzakutamandani Inu? Kodi lidzalengeza za kukhulupirika kwanu?
10. Imvani Yehova ndipo mundichitire chifundo; Yehova mukhale thandizo langa.”
11. Inu munasandutsa kulira kwanga kukhala kuvina; munachotsa chiguduli changa ndi kundiveka ndi chimwemwe,
12. kuti mtima wanga uthe kuyimbira Inu usakhale chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzapereka kwa Inu mayamiko kwamuyaya.

MIYAMBO 11:1-3
1. Muyeso wachinyengo Yehova umamunyansa, koma amakondwera ndi muyeso woyenera.
2. Kunyada kukalowa, pamafikanso manyazi, koma pamene pali kudzichepetsa pameneponso pali nzeru.
3. Ungwiro wa anthu olungama umawatsogolera, koma anthu osakhulupirika amawonongeka ndi chinyengo chawo.

MARKO 8:22-38
22. Iwo anafika ku Betisaida, ndipo anthu ena anabweretsa munthu wosaona ndipo anamupempha Yesu kuti amukhudze.
23. Iye anagwira dzanja la munthu wosaonayo napita naye kunja kwa mudzi. Atalavulira mʼmaso a munthuyo ndi kumusanjika manja, Yesu anafunsa kuti, “Kodi ukuona kalikonse?”
24. Iye anakweza maso nati, “Ndikuona anthu; akuoneka ngati mitengo imene ikuyendayenda.”
25. Kenakanso Yesu anayika manja ake mʼmaso a munthuyo. Ndipo maso ake anatsekuka, naonanso, ndipo anaona zonse bwinobwino.
26. Yesu anamuwuza kuti apite kwawo nati, “Usapite mʼmudzimo.”
27. Yesu ndi ophunzira ake anapita ku midzi yozungulira Kaisareya wa Filipo. Ali panjira, Iye anawafunsa kuti, “Kodi anthu amati ndine yani?”
28. Iwo anayankha kuti, “Ena amati Yohane Mʼbatizi; ena amati Eliya; ndipo enanso amati ndinu mmodzi wa aneneri.”
29. Iye anafunsa kuti, “Koma nanga inu, mumati ndine yani?” Petro anayankha kuti, “Inu ndinu Khristu.”
30. Yesu anawachenjeza kuti asawuze wina aliyense za Iye.
31. Iye anayamba kuwaphunzitsa kuti, “Mwana wa Munthu ayenera kumva zowawa zambiri ndi kukanidwa ndi akulu a ansembe, ndi aphunzitsi a malamulo, ndi kuti ayenera kuphedwa ndipo patatha masiku atatu adzaukanso.”
32. Izi anaziyankhula momveka bwino, ndipo Petro anamutengera pambali ndipo anayamba kumudzudzula.
33. Koma Yesu atatembenuka ndi kuyangʼana ophunzira ake, anamudzudzula Petro nati, “Choka pamaso panga Satana! Suganizira zinthu za Mulungu koma za anthu.”
34. Kenaka anayitana gulu la anthu pamodzi ndi ophunzira ake nati: “Ngati wina aliyense afuna kunditsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kunyamula mtanda wake ndi kunditsata.
35. Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine ndi cha Uthenga Wabwino, adzawupulumutsa.
36. Kodi munthu adzapindulanji akalandira dziko lonse lapansi, koma ndi kutaya moyo wake?
37. Kapena nʼchiyani chomwe munthu angapereke chosinthana ndi moyo wake?
38. Ngati wina achita manyazi chifukwa cha Ine ndi mawu anga mu mʼbado uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wa Atate ake pamodzi ndi angelo oyera.”