A A A A A

YESAYA 30:1-33
1. Tsoka kwa ana opanduka, ati Yehova, amene atenga uphungu koma si pa Ine; napangana pangano opanda mzimu wanga, kuti aonjezere tchimo ndi tchimo;
2. amene ayenda kutsikira ku Ejipito, osafunsa kukamwa kwanga, kudzilimbitsa iwo okha ndi mphamvu za Farao, ndi kukhulupirira mthunzi wa Ejipito!
3. Chifukwa chake mphamvu za Farao zidzakhala kwa inu manyazi, ndi kukhulupirira mthunzi wa Ejipito kudzakhala chisokonezo chanu.
4. Pakuti akalonga ake ali pa Zowani, ndi mithenga yake yafika ku Hanesi.
5. Iwo onse adzakhala ndi manyazi, ndi anthu amene sangapindule nao kanthu, amene sakhala kwa iwo thangata, pena phindu, koma manyazi ndi chitonzo.
6. Katundu wa zilombo za kumwera. M'dziko lovuta ndi lopweteka, kumeneko kuchokera mkango waukazi, ndi wamphongo, mphiri, ndi njoka youluka yamoto, iwo anyamula chuma chao pamsana pa abulu, ndi ang'ono zolemera zao pa malinundu a ngamira, kunka kwa anthu amene sadzapindula nao.
7. Pakuti thangata la Ejipito lili lachabe, lopanda pake; chifukwa chake ndamutcha Wonyada, wokhala chabe.
8. Tsopano pita, ukalembe mauwa pamaso pao pathabwa, nuwalembe m'buku, kuti akakhalebe kunthawi yam'tsogolo, mboni ya masiku onse.
9. Pakuti ali anthu opanduka, ana onama, ana osafuna kumva chilamulo cha Yehova;
10. amene amati kwa alauli, Mtima wanu usapenye; ndi kwa aneneri, Musanenere kwa ife zinthu zoona, munene kwa ife zinthu zamyadi, munenere zonyenga;
11. chokani inu munjira, patukani m'bande, tiletsereni Woyera wa Israele pamaso pathu.
12. Chifukwa chake atero Woyera wa Israele, Popeza inu mwanyoza mau awa, nimukhulupirira nsautso ndi mphulupulu, ndi kukhala m'menemo;
13. chifukwa chake kuipa kumeneku kudzakhala kwa inu monga pogumuka pofuna kugwa, monga potukuka m'khoma lalitali, kugumuka kwake kufika modzidzimutsa dzidzidzi.
14. Ndipo Iye adzagumulapo, monga mbiya ya woumba isweka, ndi kuiswaiswa osaileka; ndipo sipadzapezedwa m'zigamphu zake phale lopalira moto pachoso, ngakhale lotungira madzi padziwe.
15. Pakuti atero Ambuye, Yehova Woyera wa Israele, M'kubwera ndi m'kupuma inu mudzapulumutsidwa; m'kukhala chete ndi m'kukhulupirira mudzakhala mphamvu yanu; ndipo simunafuna.
16. Koma munati, Iai, pakuti tidzathawa pa akavalo; chifukwa chake inu mudzathawadi; ndipo ife tidzakwera pa akavalo aliwiro; chifukwa chake iwo amene akuthamangitsani, adzakhala aliwiro.
17. Chikwi chimodzi chidzathawa pakuwadzudzula mmodzi; pakukudzudzulani anthu asanu mudzathawa; kufikira inu mudzasiyidwa ngati mlongoti pamwamba pa phiri, ndi ngati mbendera pamwamba pa chitunda.
18. Chifukwa chake Yehova adzadikira, kuti akukomereni mtima, ndipo chifukwa chake Iye adzakuzidwa, kuti akuchitireni inu chifundo; pakuti Yehova ndiye Mulungu wa chiweruziro; odala ali onse amene amdikira Iye.
19. Pakuti anthu adzakhala m'Ziyoni pa Yerusalemu; iwe sudzaliranso, Iye ndithu adzakukomera mtima pakumveka kufuula kwako; pakumva Iye adzayankha.
20. Ndipo ngakhale Ambuye adzakupatsani inu chakudya cha nsautso, ndi madzi a chipsinjo, koma aphunzitsi ako sadzabisikanso, koma maso ako adzaona aphunzitsi ako;
21. ndipo makutu ako adzamva mau kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m'menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.
22. Ndipo mudzaipitsa chokuta cha mafano ako, osema asiliva, ndi chomata cha mafano ako osungunula agolide; udzawataya ngati kanthu konyansa, udzati kwa iwo, Chokani.
23. Ndipo Mulungu adzapatsa mvula ya mbeu yako, ukaibzale m'nthaka; ndi mkate ndiwo phindu la nthaka, ndipo tirigu wake adzacha bwino ndi kuchuluka; tsiku limenelo ng'ombe zako zidzadya m'madambo akulu.
24. Momwemonso ng'ombe ndi ana a bulu olima nthaka adzadya chakudya chochezera, chimene chapetedwa ndi chokokolera ndi mkupizo.
25. Ndipo pamwamba pa mapiri akulu onse, ndi pa zitunda zonse zazitalitali padzakhala mitsinje ndi micherenje ya madzi, tsiku lophana lalikulu, pamene nsanja zidzagwa.
26. Komanso kuwala kwake kwa mwezi kudzakhala ngati kuwala kwa dzuwa, ndi kuwala kwa dzuwa kudzakula monga madzuwa asanu ndi awiri, monga kuwala kwa masiku asanu ndi awiri, tsiku limenelo Yehova adzamanga bala la anthu ake, nadzapoletsa khana limene anawakantha ena.
27. Taonani, dzina la Yehova lichokera kutali, mkwiyo wake uyaka, malawi ake ndi akulu; milomo yake ili yodzala ndi ukali, ndi lilime lake lili ngati moto wonyambita;
28. ndi mpweya wake uli ngati mtsinje wosefukira, umene ufikira m'khosi, kupeta mitundu ya anthu ndi chopetera cha chionongeko; ndi chapakamwa chalakwitsa, chidzakhala m'nsagwada za anthu.
29. Inu mudzakhala ndi nyimbo, monga usiku, podya phwando lopatulika; ndi mtima wokondwa, monga pomuka wina ndi chitoliro, kufikira kuphiri la Yehova, kuthanthwe la Israele.
30. Ndipo Yehova adzamveketsa mau ake a ulemerero, ndipo adzaonetsa kumenya kwa dzanja lake, ndi mkwiyo wake waukali, ndi lawi la moto wonyambita, ndi kuomba kwa mphepo, ndi mkuntho ndi matalala.
31. Pakuti ndi mau a Yehova Asiriya adzathyokathyoka, ndi ndodo yake adzammenya.
32. Ndipo nthawi zonse Yehova adzawakantha ndi ndodo yosankhikayo, padzamveka mangaka ndi zeze; ndi m'nkhondo zothunyanathunyana, Iye adzamenyana nao.
33. Pakuti Tofeti wakonzedwa kale, inde chifukwa cha mfumu wakonzedweratu; Iye wazamitsapo, nakuzapo; mulu wakewo ndi moto ndi nkhuni zambiri; mpweya wa Yehova uuyatsa ngati mtsinje wa sulufure.

YESAYA 31:1-9
1. Tsoka kwa iwo amene atsikira kunka ku Ejipito kukathandizidwa, natama akavalo; nakhulupirira magaleta, pakuti ali ambiri, ndi okwera pa akavalo, pakuti ali a mphamvu zambiri; koma sayang'ana Woyera wa Israele, ngakhale kumfuna Yehova!
2. Koma Iyenso ndi wanzeru, nadzatengera choipa, ndipo sadzabwezanso mau ake, koma adzaukira banja la ochita zoipa, ndi amene athandiza iwo akugwira ntchito yoipa.
3. Koma Aejipito ndiwo anthu, si Mulungu; ndi akavalo ao ali nyama, si mzimu; ndipo pamene Yehova adzatambasula dzanja lake, wothandiza adzaphunthwa, ndi wothandizidwa adzagwa, ndipo iwo onse awiri pamodzi adzalephera.
4. Pakuti Yehova atero kwa ine, Monga mkango, ndi mwana wa mkango wobangula pa nyama yake, sudzaopa mau a khamu la abusa oitanidwa kuupirikitsa, ngakhale kudzichepetsa wokha, chifukwa cha phokoso lao; motero Yehova wa makamu adzatsikira kumenyana nkhondo kuphiri la Ziyoni, ndi kuchitunda kwake komwe.
5. Monga mbalame ziuluka, motero Yehova wa makamu adzatchinjiriza Yerusalemu; Iye adzatchinjirikiza ndi kuupulumutsa, adzapitirapo ndi kuusunga.
6. Bwerani kwa Iye amene mwampandukira kolimba, ana a Israele inu.
7. Pakuti tsiku limenelo iwo adzataya munthu yense mafano ake asiliva, ndi mafano ake agolide amene manja anuanu anawapanga akuchimwitseni inu.
8. Pamenepo Asiriya adzagwa ndi lupanga losati la munthu; ndi lupanga losati la anthu lidzammaliza iye; ndipo iye adzathawa lupanga, ndi anyamata ake adzalamba.
9. Ndipo mwala wake udzachoka, chifukwa cha mantha, ndi akalonga ake adzaopa mbendera, ati Yehova, amene moto wake uli m'Ziyoni, ndi ng'anjo yake m'Yerusalemu.

YESAYA 32:1-20
1. Taonani mfumu idzalamulira m'chilungamo, ndi akalonga adzalamulira m'chiweruzo.
2. Ndipo munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m'malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m'dziko lotopetsa.
3. Ndipo maso a iwo amene aona sadzatsinzina, ndi makutu a iwo amene amva adzamvera.
4. Mtimanso wansontho udzadziwa nzeru, ndi lilime la achibwibwi lidzalankhula zomveka msanga.
5. Wopusa sadzayesedwanso woolowa manja, ngakhale wouma manja sadzayesedwa mfulu.
6. Pakuti wopusa adzanena zopusa, ndi mtima wake udzachita mphulupulu, kuchita zoipitsa, ndi kunena za Yehova molakwira, kusowetsa konse mtima wanjala, ndi kulepheretsa chakumwa cha waludzu.
7. Zipangizonso za womana zili zoipa; iye apangira ziwembu zakuononga waumphawi ndi mau onama, ngakhale pamene wosowa alankhula zoona.
8. Koma mfulu aganizira zaufulu, nakhazikika m'zaufulu zomwe.
9. Ukani, akazi inu, amene mulinkukhala phee, mumve mau anga; inu ana akazi osasamalira, tcherani makutu pa kulankhula kwanga.
10. Pakutha chaka, kudza masiku ena inu mudzavutidwa, inu akazi osasamalira; pakuti masika a mphesa adzasoweka, sadzatuta konse.
11. Nthunthumirani, inu akazi, amene mulinkukhalaphe; vutidwani, inu osasamalira, vulani mukhale maliseche, nimumange chiguduli m'chuuno mwanu.
12. Iwo adzadzimenya pazifuwa chifukwa cha minda yabwino, chifukwa cha mpesa wobalitsa.
13. Pa dziko la anthu anga padzafika minga ndi lunguzi; inde pa nyumba zonse zokondwa, m'mudzi wokondwerera;
14. pakuti nyumba ya mfumu idzasiyidwa; mudzi wa anthu ambiri udzakhala bwinja; chitunda ndi nsanja zidzakhala nkhwimba kunthawi zonse, pokondwera mbidzi podyera zoweta;
15. kufikira mzimu udzathiridwa pa ife kuchokera kumwamba, ndi chipululu chidzasanduka munda wobalitsa, ndi munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango.
16. Pamenepo chiweruzo chidzakhala m'chipululu, ndi chilungamo chidzakhala m'munda wobalitsa.
17. Ndi ntchito ya chilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata chilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika kunthawi zonse.
18. Ndipo anthu anga adzakhala m'malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phee.
19. Koma kudzagwa matalala m'kugwa kwake kwa nkhalango; ndipo mudzi udzagwetsedwa ndithu.
20. Odala muli inu, amene mubzala m'mbali mwa madzi monse, amene muyendetsa mapazi a ng'ombe ndi bulu.

MASALIMO 108:7-13
7. Mulungu analankhula m'chiyero chake; ndidzakondwerera: ndidzagawa Sekemu; ndidzayesa muyeso chigwa cha Sukoti.
8. Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanga; ndi Efuremu ndiye mphamvu ya mutu wanga; Yuda ndiye wolamulira wanga.
9. Mowabu ndiye mkhate wanga; pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga; ndidzafuulira Filistiya.
10. Adzandifikitsa ndani m'mudzi wa m'linga? Adzanditsogolera ndani ku Edomu?
11. Si ndinu Mulungu, amene mwatitaya osatuluka nao magulu athu?
12. Tithandizeni mumsauko; pakuti chipulumutso cha munthu ndi chabe.
13. Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima: Ndipo Iye adzapondereza otisautsa.

MIYAMBO 25:23-24
23. Mphepo ya kumpoto ifikitsa mvula; chomwecho lilime losinjirira likwiyitsa nkhope.
24. Kukhala pangodya ya tsindwi kufunika kuposa kukhala m'nyumba ndi mkazi wolongolola.

2 AKORINTO 11:16-33
16. Ndinenanso, Munthu asandiyese wopanda nzeru; koma ngati mutero, mundilandirenso ine monga wopanda nzeru, kuti inenso ndidzitamandire pang'ono.
17. Chimene ndilankhula sindilankhula monga mwa Ambuye, koma monga wopanda nzeru, m'kulimbika kumene kwa kudzitamandira.
18. Popeza ambiri adzitamandira monga mwa thupi, inenso ndidzadzitamandira.
19. Pakuti mulolana nao opanda nzeru mokondwera, pokhala anzeru inu nokha.
20. Pakuti mulola ngati wina akuyesani inu akapolo, ngati wina alikwira inu, ngati wina alanda zanu, ngati wina adzikuza, ngati wina akupandani pankhope.
21. Ndinena monga mwa kunyoza, monga ngati tinakhala ofooka. Koma m'mene wina alimbika mtimamo (ndinena mopanda nzeru) momwemo ndilimbika mtima inenso.
22. Kodi ali Ahebri? Inenso. Kodi ali Aisraele? Inenso. Kodi ali mbeu ya Abrahamu? Inenso.
23. Kodi ali atumiki a Khristu? (Ndilankhula monga moyaluka), makamaka ine; m'zivutinso mochulukira, m'ndende mochulukira, m'mikwingwirima mosawerengeka, muimfa kawirikawiri.
24. Kwa Ayuda ndinalandira kasanu mikwingwirima makumi anai kuperewera umodzi.
25. Katatu ndinamenyedwa ndi ndodo, kamodzi ndinaponyedwa miyala, katatu ndinatayika posweka chombo, ndinakhala m'kuya tsiku limodzi usana ndi usiku;
26. paulendo kawirikawiri, moopsa mwake mwa mitsinje, moopsa mwake mwa olanda, moopsa modzera kwa mtundu wanga, moopsa modzera kwa amitundu, moopsa m'mudzi, moopsa m'chipululu, moopsa m'nyanja, moopsa mwa abale onyenga;
27. m'chivutitso ndi m'cholemetsa, m'madikiro kawirikawiri, m'njala ndi ludzu, m'masalo a chakudya kawirikawiri, m'chisanu ndi umaliseche.
28. Popanda zakunjazo pali chondisindikiza tsiku ndi tsiku, chalabadiro cha Mipingo yonse.
29. Afooka ndani wosafooka inenso? Akhumudwitsidwa ndani, wosatenthanso ine?
30. Ngati ndiyenera kudzitamandira, ndidzadzitamandira ndi za kufooka kwanga.
31. Mulungu Atate wa Ambuye Yesu, Iye amene alemekezeka kunthawi yonse, adziwa kuti sindinama.
32. M'Damasiko kazembe wa mfumu Areta analindizitsa mudzi wa Adamasiko kuti andigwire ine;
33. ndipo mwa zenera, mudengu, ananditsitsa pakhoma, ndipo ndinapulumuka m'manja mwake.